7 FEBRUARY, 2022
MALTA
Mboni za Yehova Zalembetsa M’kaundula wa Boma ku Malta
Bungwe latsopano la Mboni za Yehova za ku Malta (JW-Malta) lalembetsa posachedwapa m’kaundula wa boma. Pa 28 December 2021, Mboni za Yehova za ku Malta, zinapatsidwa Chikalata Chotsimikizira Dzina la Lamulo a kuti tsopano ndi bungwe lovomerezeka mogwirizana ndi malamulo a dzikolo.
Mboni za Yehova zinayamba kugwira ntchito yawo ku Malta kuyambira zaka za m’ma 1970. Ngakhale zinali choncho, kwa zaka zambiri mipingo ya Mboni za Yehova m’dzikoli, sinali yodziwika mogwirizana ndi malamulo. Chifukwa cha zimenezi, zinali zovuta kuti mipingo ikhale ndi katundu kapenanso kutsegula akaunti ku banki. Mu 1994, Bungwe la Ophunzira Baibulo Padziko Lonse (IBSA) linalembetsa ku Boma. Ngakhale kuti bungweli linali ndi mwayi wochita zinthu zina, koma silikanatha kuchita zambiri. Koma tsopano popeza bungwe la Mboni za Yehova za ku Malta, layamba kudziwika mogwirizana ndi malamulo, zikhala zosavuta kuti ofesi komanso mipingo ya Mboni za Yehova m’dzikoli, izigwira ntchito zake mosavutikira.
Ponenapo pa zomwe zachitikazi, M’bale Joe Magri amene ali m’Komiti ya Dziko la Malta anati: “Ndi zolimbikitsa kwambiri kuona mmene Yehova watidalitsira kuti tsopano tayamba kudziwika ku boma. Izi zathekanso chifukwa chothandizidwa ndi abale a m’Dipatimenti Yoona za Malamulo ku Britain komanso ku likulu la padziko lonse. Ndife osangalala kwambiri chifukwa kudziwika kwathu mogwirizana ndi malamulo, kuthandiza kuti ntchito za Ufumu zipite patsogolo komanso kuti Yehova alemekezedwe kwambiri.”
Panopo, ku Malta kuli Amboni oposa 800 omwe ali m’mipingo yokwana 11. Ndi zosangalatsa kuti ntchito ‘yolalikira za Ufumu wa Mulungu’ ku Malta, yomwe inayamba ndi mtumwi Paulo pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, ikupitiriza kupita patsogolo “popanda choletsa.”—Machitidwe 28:1, 30, 31.
a M’malamulo, mawu akuti “dzina la lamulo,” amagwiritsidwa ntchito ponena za anthu, makampani komanso mabungwe osiyanasiyana.