Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ofalitsa oposa 42,000 anadzipereka pa ntchito yayikulu yomanganso nyumba zambiri ku Central America.

APRIL 12, 2019
MEXICO

A Mboni za Yehova Amaliza Ntchito Yomanganso Nyumba Zomwe Zinaonongeka ndi Zivomezi ku Central America

A Mboni za Yehova Amaliza Ntchito Yomanganso Nyumba Zomwe Zinaonongeka ndi Zivomezi ku Central America

M’chaka cha 2017 zivomezi ziwiri zamphamvu kwambiri zinachitika ku Guatemala ndi ku Mexico. Mu December 2018 abale athu anamaliza kugwira ntchito yomanganso nyumba zonse zomwe zinaonongeka m’maderawa.

Ofesi ya nthambi ya ku Central America inayamba ntchitoyi mwa kupangitsa misonkhano ingapo yomwe cholinga chake chinali kulimbikitsa abale ndi alongo onse omwe anakhudzidwa. Misonkhanoyi inachitikira ku Chiapas, Morelos, Oaxaca, Puebla, komanso ku Mexico City. Makomiti Othandiza Pangozi Zadzidzidzi okwana 39 ndi amene anathandiza pa ntchito yomanganso nyumba zomwe zinaonongeka, potsatira malangizo a Komiti ya Nthambi.

M’bale Jesse Pérez wa m’Komiti ya Nthambi ku Central America anakumana ndi ofalitsa omwe anakhudzidwa ndi chivomezi m’dera la Morelos.

Abale awiri akugwira ntchito padenga la Nyumba ya Msonkhano yomwe inamangidwanso.

Ku Mexico, ofalitsa oposa 42,000 ochokera m’madera 10 anadzipereka kuti athandize pa ntchito yomanganso nyumba zomwe zinaonongeka. Abale ndi alongo anamanganso nyumba za abale 619, Nyumba za Ufumu 5, komanso Nyumba za Msonkhano ziwiri. Iwo anagwiranso ntchito yokonza nyumba 502 komanso Nyumba za Ufumu 53. Nyumba zokwana 10 zinamangidwanso ku Guatemala.

Ena mwa a Mboni omwe analandira thandizo anali banja la a Hernández komanso la a Santiago.

Banja la a Hernández laima kutsogolo kwa nyumba yawo yomwe inamangidwanso ndi abale ndi alongo odzipereka.

Banja la a Hernández limakhala mumzinda wa Chalco womwe uli pamtunda wa makilomita 40 kuchokera ku Mexico City. Chivomezi chomwe chinachitika pa 19 September, 2017, chinaononga kwambiri nyumba yawo. Mlongo Ana María Hernández anati: “Ngakhale kuti zinthu zinali zovuta, koma sitinasowe zinthu zofunika. Abale anatisamalira bwino kwambiri. Ndikukumbukira nthawi imene abale ndi alongo 50 kapena kuposerapo ankagwira ntchito yomanga nyumba yathu yatsopano. Anthu oyandikana nawo amadabwabe akamaona zimene abale anatichitira.” Kuonjezera pa kuwamangira nyumba, m’bale wochokera ku ofesi ya nthambi ya Central America anayendera banja la a Hernández n’kukawalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.

Banja la a Santiago laima kutsogolo kwa nyumba yawo yatsopano.

Banja la a Santiago lomwe limakhala mumzinda wa Juchitán womwe uli m’dera la Oaxaca, linakhudzidwa ndi chivomezi chomwe chinachitika pa 7 September, 2017. Chivomezicho chinaonongeratu nyumba yawo. Komabe, pasanathe miyezi 6 abale anawamangira nyumba yatsopano. Bambo wa banjali, M’bale Victor Santiago anati: “Ndinasangalala kwambiri nditaona mmene gulu la Yehova linatithandizira mwamsanga. Ndinaona kuti Yehova ankadziwa zonse zomwe tinkafunikira ndipo anatisamaliradi.”

M’bale Jesse Pérez yemwe ndi wa m’Komiti ya Nthambi ku Central America anati: “Zivomezi ziwiri zomwe zinachitika zinaononga nyumba zambiri. Komabe, ntchito yayikulu yomanganso nyumbazi inapatsa abale ndi alongo mwayi wosonyeza mtima wodzipereka. Ofalitsa ambiri anathandiza nawo pa ntchitoyi posonyeza kuti amakonda abale ndi alongo awo. Tikusangalala kuti Yehova wadalitsa ‘utumiki wothandiza’ abale athu omwe anakhudzidwa ndi zivomezi zimenezi.”—2 Akorinto 8:1-4.”