Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 23, 2021
MEXICO

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Lamasuliridwa mu Chicholi

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Lamasuliridwa mu Chicholi

Pa 20 June 2021, M’bale Robert Batko, wa m’Komiti ya Nthambi ya ku Central America, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la m’chilankhulo cha Chicholi. Baibuloli ndi la pazipangizo zamakono ndipo linatulutsidwa pa pulogalamu yochita kujambuliratu yomwe anthu pafupifupi 800 anaonera kudzera pa intaneti.

Mfundo Zina Zokhudza Ntchito Yomasulira Baibuloli

  • Chicholi ndi chilankhulo chomwe anthu a m’boma la Chiapas, kumwera chakum’mawa kwa Mexico, amalankhula

  • Anthu pafupifupi 200,000 amalankhula Chicholi

  • Ofalitsa oposa 500 amatumikira m’mipingo 22 ya Chicholi komanso m’magulu awiri

  • Omasulira atatu anagwira ntchito yomasulira Baibuloyi kwa miyezi 27

M’bale amene anathandiza nawo ntchitoyi ananena kuti: “Baibulo la dziko la tsopano lili ndi mawu ozolowereka omwe timawagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku. Ndimasangalala kwambiri ndikamawerenga chaputala chilichonse.”

M’bale winanso ananena kuti: “Ndimatha kuwerenga Baibulo mu Chisipanishi koma nditawerenga Baibulo mu Chicholi, chomwe ndi chilankhulo changa chobadwira, ndinasangalala kwambiri. Zili ngati kudya chakudya chophikidwa bwino kunyumba.”

Tikudziwa kuti Baibuloli lithandiza abale ndi alongo achilankhulochi amene akufufuza “chuma chobisika” cha m’Mawu a Mulungu Baibulo.​—Miyambo 2:4, 5.