OCTOBER 3, 2019
MEXICO
Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa M’Chizapoteki (cha ku Isthmus)
Pa 27 September, 2019, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chizapoteki (cha ku Isthmus), pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira ku San Blas Atempa, Oaxaca, m’dziko la Mexico. Pamsonkhanowu panali anthu 1,983 omwe anayamikira ndi kutulutsidwa kwa Baibuloli. M’bale Joel Izaguirre wa m’Komiti ya Nthambi ya Central America ndi amene anatulutsa Baibulo latsopanoli, lomwe ndi Baibulo la Chizapoteki (cha ku Isthmus) a loyamba kukhala ndi dzina la Mulungu lakuti Yehova.
Pa nthawi yomwe ankagwira ntchito yomasulira Baibuloli, omasulira anakumana ndi mavuto amene akanalepheretsa ntchito yawo. Atangosamukira ku ofesi ya omasulira mabuku, m’deralo munayambika zionetsero komanso zachiwawa pa zifukwa zandale. Anthu omwe ankachita zachiwawazi anatseka misewu yolowera mumzinda. Zimenezi zinachitika kwa mwezi wathunthu ndipo zinachititsa kuti chakudya chizisowa. Mwamwayi, abale athu a m’midzi yapafupi anapatsa omasulirawa zipatso ndi ndiwo zamasamba za m’minda yawo. Omasulirawa anakumananso ndi vuto lina lalikulu pamene mumzindawo munachitika chivomezi champhamvu pa 7 September, 2017. Chivomezichi chinawononga kwambiri ofesi yomwe omasulirawa ankagwiritsa ntchito moti sinalinso malo otetezeka. Mwamsanga, ofesi ya nthambi ya Central America inasamutsa omasulirawa n’kuwapititsa ku ofesi ya nthambiyi. Komanso, m’bale wa m’Bungwe Lolamulira anakonza zoti alankhulane ndi omasulira onse kudzera pa vidiyo ya pa kompyuta kuti awatonthoze komanso kuwalimbikitsa ndi mfundo za m’Baibulo.
Mosakayikira, Baibulo latsopanoli lithandiza anthu ambiri oyankhula Chizapoteki kuti ‘adziwe choonadi molondola.’—1 Timoteyo 2:3, 4.
a Chizapoteki (cha ku Isthmus) chimayankhulidwa ndi anthu oposa 85,000 a ku Mexico. Chizapoteki cha ku Isthmus ndi chimodzi mwa mitundu yosiyanasiyana yoposa 50 ya chiyankhulo cha Chizapoteki.