Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 31, 2019
MEXICO

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Latulutsidwa m’Chitsotsilu

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Latulutsidwa m’Chitsotsilu

Baibuloli linatulutsidwa pa 25 October 2019, pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira ku Chiapas, m’dziko la Mexico. Msonkhanowu unachitikira muholo ina yomwe ili mumzinda wotchedwa Tuxtla Gutiérrez ndipo M’bale Armando Ochoa, yemwe amatumikira m’Komiti ya Nthambi ya ku Central America, ndi amene analengeza za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chitsotsilu. Anthu enanso anaonera msonkhanowu muholo yotchedwa Centro de Convenciones ndipo chiwerengero chonse cha amene anaonera msonkhanowu chinali 3,747.

Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu linatulutsidwa m’Chitsotsilu pa 26 December 2014, ndipo lakhala likugawidwa kwa anthu omwe amayankhula Chitsotsilu, omwe ambiri amakhala m’mapiri komanso m’zigwa za m’chigawo cha Chiapas, ku Mexico. Pa anthu oposa 16,000,000 omwe ndi mbadwa za dziko la Mexico, pafupifupi 500,000 amayankhula Chitsotsilu, kuphatikizapo a Mboni za Yehova okwana 2,814.

Omasulira Baibuloli anakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, pali madikishonale komanso zinthu zochepa kwambiri zomwe zimapezeka m’chinenerochi. Kuwonjezera pamenepa, anthu am’madera okwanira 7 amayankhula mosiyanasiyana chinenerochi. Chifukwa cha zimenezi, omasulira amafunika kusankha mawu mosamala kwambiri kuti anthu onse omwe amayankhula chinenerochi azikamva mosavuta.

Mmodzi mwa omasulirawa anati: “Baibulo latulukali lagwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova. Zimenezi zithandiza kuti anthu amudziwe bwino Mulungu komanso akhale naye pa ubwenzi. Mabaibulo ena awiri omwe anamasuliridwa m’Chitsotsilu anatchula dzinali kamodzi kokha m’mawu am’munsi omwe amapezeka m’buku la Ekisodo. Choncho limeneli likhala Baibulo loyamba kubwezeretsa ndi dzina la Mulungu m’malo onse omwe limayenera kupezeka.” Nawonso ofalitsa omwe amayankhula Chitsotsilu amaona kuti “Mabaibulo enawo ndi odula kwambiri moti ndi ochepa omwe angakwanitse kugula. Koma Baibulo limene latulukali ndi loti munthu aliyense akhoza kulipeza kwaulere.”

Sitikukayikira kuti Baibuloli lithandiza kwambiri anthu oyankhula Chitsotsilu “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.