AUGUST 17, 2020
MEXICO
Mphepo Yamkuntho (Hurricane Hanna) Yasakaza ku Mexico
Malo
Chigawo cha Tamaulipas ndi Nuevo León ku Mexico
Ngozi yake
Pa 26 July 2020, mphepo yamkuntho (Hurricane Hanna) inawomba motsetsereka kumpoto chakum’mawa kwa Mexico ndipo inachititsa kuti madzi ambiri asefukire
Mmene mphepoyi yakhudzira abale ndi alongo athu
Ku Nuevo León, mabanja 14 anasamutsidwa m’nyumba zawo pofuna kupewa ngoziyi
Mumzinda wa Reynosa, ku Tamaulipas, ofalitsa 100 anasamuka m’nyumba zawo
Katundu amene wawonongeka
Nyumba 21 zawonongeka ku Nuevo León
Nyumba 117 zawonongeka ku Tamaulipas
Ntchito yothandiza anthu
Ofesi ya Nthambi ya Central America yakhazikitsa Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi
Oyang’anira madera ndi akulu a mipingo m’madera okhudzidwawa, akuyendetsera limodzi ntchito yoyeretsa ndi kuthira mankhwala opha majeremusi m’nyumba zomwe munalowa madzi osefukira
Ambiri mwa abale ndi alongo omwe anasamutsidwa m’nyumba zawo ku Nuevo León, panopa abwereranso kwawo
Ku Tamaulipas, abale ndi alongo am’mipingo yosiyanasiyana akupereka chakudya ndi zovala kwa anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi
Tikuthokoza Yehova chifukwa chakuti palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene wavulala pangoziyi. Ntchito yothandiza abale athu yomwe yayamba kale kuchitikayi ikusonyeza kuti nthawi zonse Atate wathu wakumwamba ndi anthu ake amakhala “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—Salimo 46:1.