NOVEMBER 28, 2014
MEXICO
Akuluakulu a Mzinda wa Mexico Anathokoza a Mboni za Yehova Chifukwa Choyeretsa Bwalo la Masewera
MEXICO CITY—Pa June 7, 2014, a Mboni za Yehova oposa 250 anadzipereka kugwira ntchito yoyeretsa bwalo la masewera lotchedwa Baldomero “Melo” Almada. Ndipo akuluakulu a boma anayamikira kwambiri zimene a Mboniwa
anachita. Bwaloli linkafunika kukonzedwa pokonzekera mwambo winawake wapadera.
Kwa miyezi yambiri, a Antonio Cota Márquez, omwe ndi oyang’anira za masewera ku Huatabampo m’dziko la Mexico, anakhala akupempha anthu kuti athandize kukonza bwalo la masewerali. Iwo ankafuna kuti ntchitoyi ichitike mwachangu kuti pa July 7, 2014, woyang’anira mzindawo adzatsegulire timisewu tatsopano tochitiramo masewera othamanga m’bwaloli. A Mboni za Yehova anavomera kuti agwira nawo ntchitoyo moti panali a Mboni ambiri amene anadzipereka. A Mboniwo anagwira ntchito yochotsa zinyalala, kupenta magolo a mpira wa basiketibo ndiponso kukonza bwalo la masewerali.
A Cota omwe tawatchula kumayambiriro aja, anaganiza zopempha a Mboni kuti athandize pa ntchitoyi chifukwa ankadziwa mmene a Mboniwa amasamalira bwaloli akamachitiramo misonkhano yawo. A Mboniwo amachita misonkhano yophunzitsa anthu Baibulo kwaulere m’bwaloli m’zinenero za Chisipanishi ndi Chimayo. Mkulu wa bomayo ataona mmene a Mboniwo anagwirira ntchito yoyeretsera bwaloli, anati: “Tasangalala kwambiri kuona anthu osadzikonda akugwiritsa ntchito nthawi yawo pokonza bwalo lathu la zamasewera.” Kenako ananena kuti: “M’malo mwa a Ramón Díaz Nieblas, omwe ndi a meya a mzinda uno, tikukuthokozani kwambiri chifukwa cha ntchito imene mwagwira lero moti tipitiriza kukulolani kuti muzichitira misonkhano yanu m’bwaloli. Tikukuthokozani chifukwa chogwira ntchito modzipereka komanso mogwirizana.”
Mungalankhule ndi:
Kuchokera M’mayiko Ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000
Mexico: Gamaliel Camarillo, tel. + 52 555 133 3000