NOVEMBER 15, 2018
MEXICO
Ngozi Zamwadzidzidzi Zikupitiriza Kuwononga Kwambiri ku Mexico
Pa 23 October, m’dziko la Mexico munachitika ngozi zamwadzidzidzi ziwiri, mvula yamphamvu yosakanikirana ndi mphepo yotchedwa Vicente, komanso mphepo yamkuntho yotchedwa Willa. Chakum’mwera kwa dzikoli, mvula ya Vicente inachititsa kuti madzi osefukira ndi matope aphe anthu okwana 11. Mphepo ya Willa inawononga kwambiri kudera la mphepete mwa nyanja ya Pacific ku Mexico komwe kunagwanso mvula yamphamvu ndipo mphepoyi inkaomba pa liwiro la makilomita 193 pa ola. Zimenezi zinachititsa kuti anthu okwana 4,250 athawe m’madera amene mphepoyi inaononga.
Ofesi ya nthambi ya Central America ndi imene imayang’anira ntchito za Ufumu m’dziko la Mexico ndipo malipoti ochokera ku nthambiyi akusonyeza kuti palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene wafa kapena kuvulala ndi mphepo zimenezi. Komabe ofalitsa 118 ku Nayarit anathawa m’nyumba zawo n’kupita kumalo okwera. Ku Sinaloa, madzi osefukira analowa m’Nyumba ya Ufumu imodzi ndi m’nyumba zambiri za abale. Madzi osefukirawa analowanso m’nyumba za mabanja 5 a Mboni ku Michoacán. Abale ndi alongo a m’maderawa ayeretsa kale nyumba komanso Nyumba ya Ufumu momwe munalowa madzi ndipo anazikonza.
Tikupempherera abale ndi alongo athu omwe anakhudzidwa ndi mphepozi ku Mexico kuti apitirize kupirira, komanso kuti azikumbukira zimene tonsefe tikuyembekezera m’tsogolo pamene ngozi zamwadzidzidzi sizidzakhalakonso.—2 Akorinto 6:4.