Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Abraham Lincoln wa m’Komiti ya Nthambi ya Micronesia, akutulutsa Baibulo la Malemba Achigiriki la Chimashalizi

MAY 24, 2019
MICRONESIA

Baibulo la Malemba Achigiriki Latulutsidwa mu Chimashalizi

Baibulo la Malemba Achigiriki Latulutsidwa mu Chimashalizi

Pa 19 May, 2019, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu mu Chimashalizi. Baibuloli linatulutsidwa pamsonkhano wapadera womwe unachitikira pa Yunivesite ya South Pacific, mumzinda wa Majuro ku Marshall Islands. Anthu ena anachita nawo msonkhanowu m’Nyumba ya Ufumu ya pachilumba cha Ebeye ndipo kuchokera ku Majuro, chilumbachi chili pamtunda woposa makilomita 440.

Anthu 339 anapezeka pamsonkhano wapaderawu kuphatikizapo ofalitsa okwana 151 omwe amasonkhana m’mipingo 4 ya ku Marshall Islands. Ofalitsawa komanso ofalitsa ena 325 omwe amatumikira m’dera la anthu oyankhula Chimashalizi ku United States, azigwiritsa ntchito Baibuloli pamisonkhano yawo, pophunzira paokha, komanso mu utumiki. Padziko lonse pali anthu pafupifupi 61,000 omwe amalankhula Chimashalizi.

M’bale wina yemwe anathandiza nawo pa ntchito yomasulira Baibuloli anafotokoza kuti: “Pa Mabaibulo onse amene akupezeka m’Chimashalizi masiku ano, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chimashalizi, ndi loyamba kubwezeretsa dzina la Yehova m’malo ake onse. Ndi Baibulo lomwe abale ndi alongo angalidalire ndipo liwathandiza kuti apitirize kukonda Yehova.”

Ndife osangalala kumva za kutulutsidwa kwa Baibulo latsopanoli. Umenewu ndi umboni wakuti Yehova akudalitsa ntchito yomasulira m’ziyankhulo zosiyanasiyana, ‘zazing’ono ndi zazikulu zomwe.’—Salimo 49:1, 2; New World Translation of the Holy Scriptures, 2013 Revision.