23 NOVEMBER 2022
MONACO
A Mboni za Yehova Avomerezedwa Mwalamulo ku Monaco
Pa 19 November 2022, a Mboni za Yehova anavomerezedwa kuti angathe kulembetsa ku boma la Monaco monga chipembedzo chovomerezeka. Zimenezi zinatheka chifukwa cha zigamulo ziwiri zokomera a Mboni za Yehova zomwe Khoti lalikulu m’dzikolo linapereka komanso chifukwa cha zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe (ECHR) linanena.
Pasanadutse zaka ziwiri kuchokera pamene abale athu anakadandaula ku khoti la ECHR, khotili linapereka maganizo ake kuboma la Monaco kuti lichitepo kanthu.
Mlandu ukangoperekedwa kuboma, choyamba mbali zonse zokhudzidwa zimapatsidwa mwayi woti zikambirane kuti zigwirizane. Pambuyo pokambirana, boma la Monaco linavomera kulembetsa a Mboni za Yehova. Pa 9 December 2021, khoti la ECHR linalemba chikalata chovomereza mgwirizano umene boma la Monaco linapanga nafe kuti litilembe kukhala chipembedzo chovomerezeka popanda kutiikira ziletso zilizonse pa kulambira kwathu. Boma linavomeranso kulipira ndalama zomwe tinawononga pa mlanduwu zoposa madola 40,000 a ku America.
Pa 16 November 2022, boma la Monaco linalemba chikalata chovomereza kulembetsedwa kwa bungwe la Monaco Association for the Worship of Jehovah’s Witnesses (Association Monégasque pour le Culte des Témoins de Jéhovah). Chikalatacho anachiika m’magazini yofotokoza malamulo a ku Monaco pa 18 November 2022.
Tikusangalala kuti abale ndi alongo athu ku Monaco tsopano akulambira Yehova popanda kuletsedwa ndi boma. Tikuthokozanso Yehova chifukwa tavomerezedwa mwalamulo kuti tizitha kumulambira pambuyo podikira nthawi yaitali.—Afilipi 1:7.