Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale ndi alongo limodzi ndi maloya oimira Mboni za Yehova ali panja pa khoti mumzinda wa Ulaanbaatar lomwe ndi likulu la dziko la Mongolia.

AUGUST 24, 2018
MONGOLIA

A Mboni za Yehova Awina Mlandu ku Mongolia Ndipo Alembetsanso Monga Chipembedzo Chovomerezeka ndi Boma

A Mboni za Yehova Awina Mlandu ku Mongolia Ndipo Alembetsanso Monga Chipembedzo Chovomerezeka ndi Boma

Pa 14 June, 2018, a Mboni za Yehova mumzinda wa Ulaanbaatar womwe ndi likulu la dziko la Mongolia, anapatsidwa satifiketi yatsopano kuchokera ku ofesi yoyang’anira mzindawu yosonyeza kuti chipembedzo chawo n’chovomerezeka ndi boma.

Satifiketi yatsopano yosonyeza kuti a Mboni za Yehova ndi ovomerezeka ndi boma kuti azigwira ntchito zawo ku Ulaanbaatar.

Malamulo a dziko la Mongolia amafuna kuti zipembedzo zizilembetsedwa ku boma chaka chilichonse, ndipo abale athu akhala akuchita zimenezi kungoyambira pamene analembetsa koyamba mu 1999. Komabe, mu 2015 ofesi yoyang’anira mzinda wa Ulaanbaatar inakana kuti a Mboni za Yehova alembetse. Kenako mu January 2017, ofesi yoyang’anira mzindayo inapereka chigamulo chomwe chinachititsa kuti a Mboni za Yehova asakhalenso ndi ufulu wochita zinthu zokhudza kulambira. Oimira ofesiyi anakana kusonyeza umboni umene unawachititsa kupereka chigamulo chimenechi. Abale anaganiza zokasuma nkhaniyi kukhoti.

Pamene khoti linkazenga mlanduwu, loya woimira ofesiyo anafotokoza kuti apereka chigamulocho potengera zimene Khoti Lalikulu Kwambiri m’dziko la Russia linagamula kuti malo onse ovomerezeka a Mboni za Yehova m’dzikolo atsekedwe. Maloya athu anatsutsa zimenezi ponena kuti mayiko ambiri anadzudzula boma la Russia chifukwa cha zimene linachitazi ndipo makhoti ambiri ananena kuti zimenezi n’zosemphana ndi malamulo. Kuonjezera pamenepa, khotili analikumbutsa kuti chigamulo cha ku Russia chinali chisanapangidwe pamene khotili limapereka chigamulo chakechi ndiye n’zosamveka kuti ofesiyi inapanga chigamulo chake chifukwa cha zimene zinachitika ku Russia.

Khoti lomwe linkazenga mlanduwu linasintha chigamulo chomwe ofesi yoyang’anira mzinda ija inapanga, ndipo linanena kuti ofesiyo inangochita zinthu pogwiritsa ntchito mphekesera komanso kuti inalephera kupereka umboni wosonyeza kuti a Mboni amachita zinthu zoipa. Khotilo linapezanso kuti ofesiyo inaphwanyira abale ufulu umene munthu aliyense ali nawo, kuphatikizapo ufulu wochita zinthu zokhudza chipembedzo chako kapena zimene umakhulupirira.

A Jason Wise, omwe ndi mmodzi mwa anthu amene anali maloya a Mboni pa mlanduwu anati: “Ngakhale kuti kukhala ndi maufulu osiyanasiyana sikudalira kuti munthu ukachite kulembetsa ku boma, nthawi zambiri zimakhala zovuta kulambira mwaufulu ngati simunalembetse. Kulembetsa ku boma kumathandiza kuti tiziitanitsa Mabaibulo komanso zinthu zina zofotokoza Baibulo kuchokera ku mayiko ena, kukhala ndi malo athu olambirira, komanso kupanga lenti malo ochitira misonkhano ikuluikulu. Ndife osangalala kuti khoti lasintha chigamulo chomwe ofesi ya mumzinda wa Ulaanbaatar inapanga ndipo linazindikira kuti zimene ofesiyi inachita zisokoneza ufulu wathu wopembedza komanso wosonkhana pamodzi ku Mongolia.”