APRIL 21, 2021
MYANMAR
Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2021—Myanmar
Nkhani ya Chikumbutso Inakambidwa pa Nthawi ya Ziwawa Kudzera pa Telefoni
Kuyambira mu February 2021, m’dziko la Myanmar mwakhala mukuchitika ziwawa. Kutatsala ma wiki ochepa kuti mwambo wokumbukira imfa ya Khristu uchitike, anthu anayamba kumenyana m’madera osiyanasiyana m’dzikoli. Zimenezi zinachititsa kuti ofalitsa ambiri pa ofalitsa 5,102 omwe ali m’dzikoli azilephera kugwiritsa ntchito Intaneti. Choncho abale anamvetsera nkhani ya Chikumbutso kudzera pa telefoni.
Mu mzinda wina, pa tsiku la Chikumbutso, anthu anayamba kuwomberana kwambiri m’misewu. Asilikali anayamba kuyenda nyumba iliyonse kufufuza anthu amene ankachita ziwonetsero. Pa nthawiyi, abale analimbikitsidwa ndi mawu a mu lemba lachaka chino la Yesaya 30:15 kuti ayenera ‘kukhala osatekeseka ndi kukhulupirira Yehova.’ Abalewa anabisala m’nyumba zawo ndipo anaonetsetsa kuti asamalankhule mokweza komanso kuti m’nyumbamo musamawale kwambiri moti anachita mwambo wa Chikumbutso popanda mavuto ena alionse. Ngakhale kunali ziwawa, pa mwambowu panapezeka anthu ambiri kuposa m’mbuyo monsemu. Ambiri anamvetsera nkhaniyi kudzera pa telefoni.
Anthu amene anapezeka pa mwambo wa Chikumbutso m’dzikoli, analipo 11,877. Chiwerengerochi chinaposa cha mu 2019 ndi 14 peresenti.
Tili ndi chikhulupiriro kuti Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, amasangalala akamaona abale akupitirizabe kumulambira molimba mtima ngakhale pa nthawi imene kukuchitika ziwawa.—Miyambo 27:11.