Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 10, 2016
NAGORNO-KARABAKH

Mnyamata Wina ku Nagorno-Karabakh Anamangidwa Atakana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Mnyamata Wina ku Nagorno-Karabakh Anamangidwa Atakana Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Artur Avanesyan yemwe ndi mnyamata wa zaka 20, akugwira ukaidi wa miyezi 30 m’ndende ya Shushi ku Nagorno-Karabakh atakana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Iye anamangidwa ngakhale kuti anali wokonzeka kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Makhoti onse a ku Nagorno-Karabakh anakana kuvomereza ufulu wofunika kwambiri umene Artur ali nawo wokana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Artur, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, anafotokoza zinthu zimene amazikhulupirira kwambiri. Iye anati: “Sindingagwire ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene ndimaphunzira m’Baibulo. Ndimakonda munthu wina aliyense ndipo sindinganyamule zida za nkhondo kapena kuphunzira mmene ndingavulazire anthu ena.” Iye ananenanso kuti: “Sikuti ndikuzemba udindo wanga wogwira ntchito zothandiza dziko langa. Ndinayesetsa kupempha kuti ndipatsidwe ntchito zina m’malo mwa usilikali, koma sindinaloledwe.”

Sanaloledwe Kugwira Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali

Pa 29 January, 2014, Artur analandira uthenga woti apite ku dipatimenti ina ya asilikali m’tauni ya Askeran ku Nagorno-Karabakh. Tsiku lotsatira, iye anakapereka kalata yofotokoza kuti sangagwire ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira komanso kuti anali wokonzeka kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Artur anapemphanso loya kuti amuthandize pa nkhaniyi chifukwa ankadziwa kuti m’dziko la Nagorno-Karabakh mulibe lamulo loti anthu amene sakufuna kugwira ntchito ya usilikali azipatsidwa ntchito zina.

Chifukwa chakuti Artur ndi nzika ya dziko la Armenia, loya wake anakumana ndi akuluakulu a boma la Armenia komanso a dziko la Nagorno-Karabakh ndipo zinkaoneka ngati Artur akhoza kuloledwa kumakagwira ntchito zosakhudzana ndi usilikali m’dziko la Armenia. Chifukwa cha zimenezi, iye anasamukira ku Armenia. Pa 13 February, 2014, iye anakapereka kalata ku dipatimenti ina ya asilikali ku Armenia yopempha kuti apatsidwe ntchito zina m’malo mwa usilikali.

Nthambi imene imapereka ntchito zosakhudzana ndi usilikali ku Armenia, sinamuyankhe chilichonse. M’malomwake, pa 14 July, 2014, a polisi mu mzinda wa Yerevan m’dziko la Armenia, anamuuza kuti apite ku likulu la apolisi kumene a polisi a ku Nagorno-Karabakh ankamuyembekezera. Atafika, mwamsanga apolisiwo anamumanga ndipo kenako anabwerera naye ku Askeran m’dziko la Nagorno-Karabakh kuti akamuzenge mlandu. Apolisiwo nachita zimenezi mom’kakamiza, asanamuzenge mlandu uliwonse, popanda kulamulidwa ndi khoti ndipo sanatsatire dongosolo lililonse.

Kumangidwa Komanso Kuzengedwa Mlandu

Artur anagona m’ndende kwa nthawi yoyamba pa 14 July, 2014 ndipo pa nthawiyo anali ndi zaka 18 zokha. Tsiku lotsatira anamutengera ku khoti ndipo kumeneko iye anazindikira kuti khotilo, lomwe ndi laling’ono ku Nagorno-Karabakh, ndi limene linalamula kuti amutsekere m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu. Khotilo linabwerezanso kunena kuti Artur akhale m’ndende poyembekezera kumuzenga mlandu ndipo anaikidwa m’ndende ya Shushi. Iye anapanga apilo kangapo chifukwa anaikidwa m’ndende asamuzenge mlandu, koma ma apilo onse anakanidwa.

Pa 30 September, 2014, a Spartak Grigoryan, omwe ndi woweruza milandu pa khoti laling’onolo, analamula Artur kuti akakhale m’ndende kwa miyezi 30 pa mlandu wozemba ntchito ya usilikali. a Artur anapanga apilo za nkhaniyi koma Khoti la Apilo komanso Khoti Lalikulu m’dzikolo anamupezabe wolakwa pa mlanduwu. Iye adzatuluka m’ndende mu January 2017.

Sanasinthe Maganizo Ngakhale Kuti Anamuchitira Zopanda Chilungamo

A Shane Brady, omwe ndi mmodzi wa maloya a Artur, ananena kuti: “Artur anasungidwa ndi apolisi, kumangidwa, kuzengedwa mlandu komanso kumupeza wolakwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti anamangidwa mopanda chilungamo, iye watsimikiza mtima kuti sangagwire ntchito ya usilikali.” A Brady ananena kuti panopo akuluakulu a ndende anamulola Artur kuti akhoza kukhala ndi Baibulo, mabuku othandiza kuphunzira Baibulo komanso kuti achibale ake angathe kumadzamuona ku ndendeko.

Artur anakasuma za nkhaniyi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya makhoti onse a m’dziko lake atalephera kumuthandiza. Iye akukhulupirira kuti Khotili ligamula bwino nkhaniyi chifukwa kwa nthawi yayitali ilo lakhala likunena kuti munthu ali ndi ufulu wokana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Komabe Khotilo lingadzapereke chigamulo chake pambuyo poti Artur watuluka m’ndende. Pa mlandu wa a Bayatyan ndi Dziko la Armenia, Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya inanena kuti munthu angathe kukana ntchito ya usilikali chifukwa ali ndi ufulu wotsatira maganizo ake, zimene amakhulupirira komanso chipembedzo chake. Khotili lakhala likubwereza mfundo imeneyi mu zigamulo zinanso zokhudza milandu ya anthu amene anakana kulowa usilikali. b

Zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lakhala likugamula, zathandiza kuti mayiko azilemekeza ufulu umene munthu ali nawo wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ngakhale pamene m’dzikomo muli ziwawa kapena nkhondo. Mwachitsanzo, mu June 2015, khoti lalikulu m’dziko la Ukraine linavomereza kuti anthu ali ndi ufulu wokana kugwira ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene makhulupirira, ndipo linanena kuti anthuwo azipatsidwa ntchito zina.

Kodi Anthu a ku Nagorno-Karabakh Amene Safuna Kugwira Ntchito ya Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira Ayembekezere Kuti Zinthu Zisintha?

A Mboni za Yehova ku Nagorno-Karabakh komanso pa dziko lonse, akukhulupirira kuti dziko la Nagorno-Karabakh liyamba kuona ufulu umene munthu ali nawo wokana ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira monga chinthu chofunika kwambiri. Kodi dzikolo lizipereka ntchito zina kwa anyamata okonda mtendere omwe sakufuna kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira m’malo mowamanga? Ngati dziko la Nagorno-Karabakh lingavomereze ufulu wokana usilikali umene munthu ali nawo, zingakhale zogwirizana ndi mfundo zovomerezeka zimene mayiko a ku Ulaya amayendera. Komanso zimenezi zingasonyeze kuti dzikoli likulemekeza kwambiri zimene anyamata monga Artur amakhulupirira.

a Chilango cha Artur Avanesyan choti akhale m’ndende kwa miyezi 30 chinayamba pamene anamangidwa pa 14 July, 2014.

b Onani milandu ya pakati pa a Erçep ndi Dziko la Turkey, nambala 43965/04, 22 November 2011; a Feti Demirtaş ndi Dziko la Turkey, nambala 5260/07, 17 January 2012; a Buldu Komanso Anzawo ndi Dziko la Turkey, nambala 14017/08, 3 June 2014.