Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NAMIBIA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Namibia

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Namibia

A Mboni za Yehova akhala akupezeka ku Namibia kuyambira mu 1929. Komabe, ulamuliro wosankhana mitundu wa dziko la South Africa womwe unkalamulira dziko la Namibia mochita kulamulidwa ndi bungwe la League of Nations, unkaletsa ntchito zawo. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1950 mpaka chakumapeto kwa zaka za m’ma 1970, akuluakulu a boma sankalola kuti azungu azipezeka kumalo omwe kunkakhala anthu akuda popanda kupatsidwa chilolezo ndi boma, ndipo zimenezi zinkachititsa kuti amishonale ochokera m’mayiko ena asamagwire bwino ntchito yawo. Pa nthawiyo, a Mboni ankatsutsidwa kwambiri ndi atsogoleri a zipembedzo komanso akuluakulu a boma pa ntchito yawo youza ena zimene amakhulupirira.

Pa 21 March, 1990, dziko la Namibia linalandira ufulu wodzilamulira. Pa malamulo atsopano omwe dzikoli linayamba kuyendera, a Mboni za Yehova anakhala ndi ufulu wambiri pa ntchito yawo. Mu 2008, iwo analembetsa ku boma monga chipembedzo chovomerezeka. A Mboni za Yehova ku Namibia akuyamikira chifukwa ali ndi ufulu wochita zinthu zosiyanasiyana zokhudza chipembedzo chawo.