Pitani ku nkhani yake

17 JUNE, 2015
NEPAL

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Okhudzidwa ndi Chivomerezi ku Nepal

A Mboni za Yehova Akuthandiza Anthu Okhudzidwa ndi Chivomerezi ku Nepal

MZINDA WA KATHMANDU, ku Nepal—Pa 25 April, 2015, m’dzikoli munachitika chivomerezi champhamvu chomwe chinapha anthu masauzande ambiri kuphatikizapo wa Mboni mmodzi ndi ana ake awiri. Izi zitachitika, a Mboni za Yehova a ku Bangladesh, Germany, India, Japan, Switzerland komanso a ku United States anayamba kuthandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi. Kenako m’dzikoli munachitikanso chivomerezi china pa 12 May, 2015. Koma pa ulendo wachiwiriwu, a Mboni za Yehova anazindikira kuti palibe wa Mboni amene anamwalira, kuvulala kapena katundu wake anawonongeka kwambiri.

A Mboni za Yehova akugawira chakudya anzawo komanso anthu ena omwe anakhudzidwa ndi chivomerezi.

Chivomerezi choyamba chija chitachitika, tsiku lotsatira, anthu ena ochokera ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dzikoli anayendera mipingo ya m’dera la Kathmandu. Mipingo ya m’derali ndi imene inakhudzidwa kwambiri ndi chivomerezichi. Nyumba za a Mboni 38 zinagweratu ndipo zina 126 zinawonongeka. A Mboni amene nyumba zawo zinagweratu anayamba kusungidwa ndi a Mboni anzawo ndipo ena anayamba kukhala mu Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova. Ena ankakhala m’matenti omwe anamangidwa m’malo ena. Ofesi ya Mboni za Yehova ya ku Nepal inayamba kugawa chakudya kwa anthuwa. Chakudyachi chinkachokera ku Bangladesh, India komanso m’mizinda ina ya m’dziko la Nepal monga Birgunj, Damauli, Mahendranagar ndi Pokhara. Komiti yopereka chithandizo pakagwa zamwadzidzidzi ndi imene ikuyang’anira ntchito ya a Mboni ongodzipereka ochokera ku India, Japan ndiponso ku Nepal omwe akumanga nyumba zoyembekezera za anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Anthu ongodzipereka a ku nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Nepal akulandira zakudya zochokera mumzinda wa Birgunj.

Wolankhula m’malo mwa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Nepal, dzina lake Reuben Thapaliya, anati: “Sikuti tikungofuna kuthandiza anthuwa ndi zakudya, madzi ndi malo okhala basi. Tikufunanso kuwalimbikitsa ndi Mawu a Mulungu. Choncho takonza zoti tikathandize anthu pa zinthu zonsezi.” Pa 2 mpaka pa 5 May, 2015, woimira likulu la Mboni za Yehova la padziko lonse, dzina lake Gary Breaux, anayendera madera onse amene akhudzidwa ndi ngoziyi. Anayenderanso mipingo ndiponso mabanja a Mboni za Yehova. Ndiyeno pa 4 May, 2015, a Breaux anakamba nkhani yapadera kuchokera m’Baibulo. Anthu a m’mipingo ina ya m’deralo anaonera nkhaniyi kudzera pa Intaneti. Komanso woimira ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Japan, dzina lake Kenji Chichii, anafika m’dzikoli pa 5 May, 2015. Nayenso anayendera mabanja a m’derali ndiponso anakamba nkhani zolimbikitsa zochokera m’Baibulo.

Woimira likulu la Mboni za Yehova padziko lonse, dzina lake Gary Breaux (kumanja), akuyendera nyumba ina yomwe inagumuka.

Ofesi ya nthambi ya ku Germany inatumiza dokotala, nesi ndi anthu ena odziwa zachipatala. Anthuwa anagwira ntchito limodzi ndi a m’komiti yopereka chithandizo aja kuti akathandize anthu ovulala omwe ankasungidwa mu Nyumba za Ufumu. Iwo anagwiritsa ntchito mankhwala omwe anthu a ku Bangladesh, India ndi Japan anapereka komanso zipangizo zina zachipatala.

Gulu la anthu othandiza pangozi likugwira ntchito mu Nyumba ya Ufumu ya ku Kathmandu ndipo a Mboni amene akhudzidwa ndi ngoziyo akuwapatsa chakudya.

Wolankhula m’malo mwa likulu la Mboni za Yehova padziko lonse, dzina lake J. R. Brown, anati: “Tipitirizabe kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngoziyi chifukwa pali zambiri zimene anthuwa akufunikira. A Mboni anzathu ku Nepal ndiponso anthu ena amene anakhudzidwa ndi ngoziyi ayenera kudziwa kuti tipitirizabe kuwathandiza ndi zofunika pa moyo komanso kuwalimbikitsa ndi Mawu a Mulungu. Tipitiriza kuwaganizira ndiponso kuwapempherera.”

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: J. R. Brown, Ofesi ya Nkhani, tel. +1 718 560 5000

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110

Japan: Ichiki Matsunaga, tel. +81 46 233 0005

Nepal: Reuben Thapaliya, tel. +977 9813469616