Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’mwamba: Beteli ya ku Amsterdam mu 1964. Mmunsi: Abale ndi alongo ogwira ntchito pa Beteli cha m’ma 1950 ndi 1960

7 OCTOBER, 2022
NETHERLANDS

Zaka 100 Zomwe Tinakumana Ndi Mavuto Komanso Zinthu Zosangalatsa ku Netherlands

Zaka 100 Zomwe Tinakumana Ndi Mavuto Komanso Zinthu Zosangalatsa ku Netherlands

Chaka chino cha 2022, ofesi ya nthambi ya Amsterdam komwe ndi ku likulu kwa dziko la Netherlands, yakwanitsa zaka 100 kuyambira pomwe inakhazikitsidwa. Kungoyambira nthawi imeneyo, abale ndi alongo athu akhala akusonyeza chikhulupiriro cholimba.

Uthenga wabwino unafika ku Netherlands chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, pamene mnyamata wina dzina lake Heinrich Brinkhoff anayamba kuwerenga mabuku ofalitsidwa ndi a Watch Tower Society komanso Bungwe la Ophunzira Baibulo Padziko Lonse. Patangodutsa nthawi yochepa, iye anayamba kuuza ena zimene ankaphunzirazo ndipo mbewu za choonadi zinayamba kukula. Mu 1920, M’bale Joseph F. Rutherford anapita ku Europe ndipo anakakhazikitsa ofesi ya nthambi ku Switzerland. Ofesiyi ndi yomwe inkayang’aniranso ntchito yathu ku Netherlands. Mu 1921, M’bale Rutherford anasankha M’bale Adriaan Block kuti azikayang’anira ntchito ku Netherlands. Mu 1922, ofesi ya nthambi inakhazikitsidwa ku Amsterdam.

Ofesi ya nthambiyi itayamba kugwira ntchito ku Amsterdam, ntchito yolalikira inayamba kuyenda bwino. Chiwerengero cha atumiki a Yehova chinapitirizabe kukula kwambiri. Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itatsala pang’ono kuyamba, m’dzikoli munali ofalitsa pafupifupi 500 omwe ankalalikira mwakhama.

Nkhondoyi itayamba, chipani cha Nazi chinayamba kulamulira ku Netherlands. Chipanichi chinayamba kuzunza a Mboni za Yehova komanso magulu ena a anthu. Panthawiyi, a Mboni okwana 300 olankhula Chidatchi anawasamutsira m’madera ena ndipo ambiri anawapititsa ku ndende zozunzirako anthu. Abale athu pafupifupi 130 anafa ndi matenda komanso chifukwa cha mavuto ena. Ngakhale kuti iwo ankazunzidwa, pomwe nkhondo inkatha mu 1945, chiwerengero cha a Mboni ku Netherlands chinafika pa 3,125.

Komabe ngakhale nkhondoyi inali itatha, koma mavuto sanathere pomwepo. Tchalitchi cha Katolika chinkatsutsa kwambiri a Mboni makamaka m’chigawo cha kum’mwera kwa dzikoli. Chitsanzo chimodzi ndi zomwe zinachitika mu 1952, pomwe a tchalitchichi ankafuna kulepheretsa msonkhano ku Venlo. Zimenezi zinachititsa kuti mwiniwake wa malo omwe tinachita lendi kuti tichitirepo asinthe maganizo kuti tisagwiritsenso ntchito malowo kuchitirapo msonkhano wachigawo. Komabe zimenezi sizinafooketse abale, iwo anangopezanso malo ena pomwe anakakungapo tenti n’kuchitabe msonkhanowo.

Otsutsawo sanasiyire pomwepo. Nthawi ina pa msonkhano wachigawo, pa chigawo cha lamlungu masana kunabwera anthu oposa 1,000 kuti adzasokoneze msonkhanowo. Kenako kunabweranso apolisi omwe anadzamanga abale ena msonkhano uli mkati.

Ofesi ya nthambi yomwe ili ku Emmen panopa

Zolinga za anthu otsutsawo sizinaphule kanthu. Potsatira malangizo omwe tinapatsidwa ndi ofesi ya nthambi, abale anapitiriza kuchititsa msonkhanowu.

Yehova anapitiriza kudalitsa abalewa chifukwa cha khama lawo. Mu 1983, nthambi ya Netherlands anaisamutsira ku maofesi atsopano ku Emmen. Pofika mu 2022, chiwerengero cha a Mboni za Yehova ku Netherlands chikukwana pafupifupi 30,000.

Mbiri ya Mboni za Yehova ku Netherlands ikutitsimikizira kuti Yehova ‘sadzataya kapena kusiya ngakhale pang’ono’ anthu ake.​—Deuteronomo 31:6.