AUGUST 8, 2019
NETHERLANDS
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Utrecht, Netherlands
Masiku: 2 mpaka 4 August, 2019
Malo: Jaarbeurs Hallencomplex, Utrecht, Netherlands
Zinenero: Chiarabu, Chidatchi, Chinenero Chamanja cha ku Netherlands, Chingelezi, Chipapiamento, Chipolishi, Chipwitikizi, Chisipanishi, Chitwi
Chiwerengero cha Osonkhana: 42,335
Chiwerengero cha Obatizidwa: 212
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,000
Nthambi Zoitanidwa: Australasia, Belgium, Brazil, Canada, Colombia, Indonesia, Korea, Portugal, Romania, South Africa, Suriname, ndi United States
Zina Zomwe Zinachitika: M’bale wina amagwira ntchito ku kampani ina yoyeretsa malo ndipo kampaniyo inapeza ntchito yoyeretsa malo a Jaarbeurs Hallencomplex. M’baleyo analandira foni kuchokera kwa abwana ake ndipo anamuuza kuti: “Tsopano tili ndi gulu la anthu omwe akuchita zonse zomwe tinagwirizana ndipo akuzichita pa nthawi yake. Akuyeretsa malowa ndipo apanga dongosolo lawo loyeretsera kuti pasapezeke pena paliponse posayeretsedwa. Sitikukayika kuti malowa awasiya ali abwino kwambiri kuposa mmene analili pamene tinkawapatsa kuti ayambe kuwagwiritsa ntchito. N’zochititsa chidwi kwabasi! Zimenezi sindinazionepo. Ayeretsa ngakhale mbali ina ya lesitilanti yomwe panopa sikugwiritsidwa ntchito. Nthawi zonse kuzimbudzi kukumakhala anthu awiri omwe akumathandiza anthu, ndipo ngati penapake pali vuto, nthawi yomweyo anthu amabwera kudzakonza. Sindinaonepo zimenezi zikuchitika.”
Abale ndi alongo a ku Netherlands akulandira alendo ochokera kumayiko ena
Atumiki a pa Beteli akulandira alendo omwe abwera kudzaona nthambi ya Netherlands
Mlongo wochokera kudziko lina akugwira ntchito yoitanira anthu kumsonkhano limodzi ndi mlongo wa ku Netherlands
Abale ndi alongo akumvetsera msonkhano mu holo yaikulu ya Jaarbeurs Hallencomplex. Abale ndi alongo ena anaonera msonkhanowu m’maholo enanso 5 a pamalopa
Ena mwa abale ndi alongo 212 atsopano akubatizidwa
Abale ndi alongo akumvetsera nkhani ndiponso akulemba notsi
Alendo ochokera kumayiko ena akupatsana mphatso
M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira, akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Lamlungu
Amishonale ndiponso atumiki ena anthawi zonse akubayibitsa anthu pamapeto pa msonkhano