NOVEMBER 15, 2016
NEW ZEALAND
Ku New Zealand Kunachitika Chivomerezi Champhamvu 7.8 komanso Zivomerezi Zina Zing’onozing’ono
Pakati pa usiku wa Lolemba, 14 November, 2016, pa chilumba chomwe chili kum’mwera kwa dziko la New Zealand panachitika chivomerezi champhamvu 7.8. Malipoti akusonyeza kuti anthu awiri anaphedwa ndi chivomerezicho. Kuchokera panthawiyi, pachilumbachi pakhala pakuchitika zivomerezi zina zing’onozing’ono zambiri komanso zina zamphamvu 6.0 kapena kuposa. Zivomerezi zimenezi zinachititsa kuti nyumba zigwe, komanso zinawononga njanji, misewu, mapaipi a madzi ndiponso mapaipi odutsa zinthu zonyansa. Zinachititsanso kuti kukhale kopanda magetsi ndi intaneti.
Malinga ndi zimene akulu a m’mipingo ya ku New Zealand komanso ofesi ya Mboni za Yehova ku Australia inafotokoza, palibe wa Mboni amene anavulala kapena kuphedwa ndi chivomerezicho. A Mboni za Yehova anakhazikitsa komiti yopereka chithandizo pakagwa ngozi zamwadzidzidzi mu mzinda wa Christchurch womwe uli pamtunda wa makilomita 91, kum’mwera kwa malo omwe kunayambira chivomerezicho. Ngakhale kuti nyumba zochepa za anthu a Mboni komanso malo awo olambirira zinawonongeka, komitiyi inayesetsa kusamalira komanso kuthandiza anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi kuti akhalebe paubwenzi wabwino ndi Mulungu.
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ku New York, ndi limene linkayang’anira ntchito yopereka chithandizo. Ngati patafunika bungweli limatha kulola komiti yopereka chithandizo kuti igwiritse ntchito ndalama zomwe anthu amapereka mwakufuna kwawo pofuna kuthandiza ntchito yolalikira padziko lonse.
Lankhulani ndi:
Padziko lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000
Australia ndi New Zealand: Rodney Spinks, 61-2-9829-5600