8 APRIL, 2021
NIGERIA
A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso M’chilankhulo cha Chiibo
Pa 4 April 2021, M’bale Kenneth Cook, wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’Chiibo pa msonkhano wochita kujambula. Ofalitsa m’mipingo yoposa 1,140 ya chilankhulochi anasangalala kwambiri kulandira Baibulo lokonzedwanso. Papita zaka 14 kuchokera pamene ofalitsawa analandira koyamba Baibulo la Dziko Latsopano m’Chiibo.
Baibulo limeneli lidzathandiza ofalitsa oposa 50,000 amene ali m’gawo lolankhula Chiibo. Lidzakhala lothandizanso kwambiri polalikira kwa anthu oposa 40 miliyoni amene amalankhula chilankhulochi.
M’bale wina wogwira ntchito yomasulira m’chilankhulochi ananena kuti: “Kuika mawu am’munsi ambiri mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso kudzathandiza kuti munthu aliyense amene amalankhula chilankhulochi azikonda kuliwerenga. Sikuti mawu am’munsi amangofotokoza matanthauzo a mawu a Chiheberi ndi Chigiriki basi. Koma amasonyezanso mawu a Chiibo ofanana ndi amene agwiritsidwa ntchito ndipo izi zimathandiza kuti ngakhale anthu amene amalankhula chilankhulochi mosiyanako azimvabe akamawerenga.”
M’bale Archibong Ebiti, wa mu Komiti ya Nthambi ku Nigeria anati: “Omasulira 6 anagwira ntchito kwa zaka 4 kuti amalize kukonza Baibuloli. Ngakhale kuti mliriwu unabweretsa mavuto ena osayembekezereka, timathokoza Yehova kuti anapereka mzimu woyera mowolowa manja kwa anthu onse amene ankagwira ntchitoyi.”
Sitikukayikira kuti a Mboni onse olankhula Chiibo padziko lonse adzasangalala kuwerenga mawu osangalatsa a m’Baibulo lokonzedwansoli. Zidzakhalanso zosavuta kuti aziligwiritsa ntchito pophunzitsa komanso kufotokozera anthu ena “njira ya Mulungu.”—Acts 18:26.