28 DECEMBER 2023
NIGERIA
Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu Latulutsidwa mu Chiedo ndi Chiesani
Milungu iwiri yotsatizana, abale omwe amatumikira mu Komiti ya Nthambi ku Nigeria anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu m’zinenero ziwiri za m’dzikoli. Mabaibulowa anatulutsidwa pa Msonkhano Wachigawo wa chaka cha 2023, wamutu wakuti “Khalani Oleza Mtima” womwe unachitikira ku Benin City ndi ku Agbor, m’dziko la Nigeria. Pa 8 December 2023, M’bale Archibong Ebiti anatulutsa Baibulo la Malemba Achigiriki mu Chiedo. Kenako pa 15 December 2023, M’bale Malcolm Hall anatulutsa Baibuloli mu Chiesani. Pamisonkhano yonse iwiriyi anthu analandira Mabaibulo osindikizidwa. Mabaibulowa anatulukanso apazipangizo zamakono.
Chiedo
Anthu okwana 1,678 anasonkhana pa nthawi imene Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu linkatulutsidwa mu Chiedo. Zikuoneka kuti pali anthu pafupifupi 2 miliyoni omwe amalankhula Chiedo padziko lonse. Abale ndi alongo opitirira 900 amatumikira m’mipingo ya Chiedo ku Nigeria. Gulo la omasulira Chiedo linayamba kugwira ntchito yomasulira mu 2014. Mabuku a chinenerochi anayamba kupezeka pawebusaiti yathu ya jw.org m’chaka chimenechi.
Ngakhale kuti Mabaibulo ena a Chiedo alipo, koma ndi zovuta kuwapeza komanso ndi odula kwambiri. Dzina la Yehova linachotsedwa m’Mabaibulo ambiri a Chiedo ndipo ali ndi mawu ovuta zomwe zimachititsa kuti anthu oyankhula Chiedo azivutika kumvetsa uthenga wa m’Baibulo. Mlongo Patience Izevbuwa, wazaka 74, yemwe wakhala akutumikira Yehova kwa zaka 50 ananena kuti: “Ndasangalala kwambiri kuti tsopano tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu mu Chiedo. Chimwemwe changa ndi chosaneneka!”
Chiesani
Anthu okwana 692 anasonkhana pa nthawi imene Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu linkatulutsidwa mu Chiesani. Anthu opitirira 1 miliyoni amayankhula Chiesani ku Nigeria. Panopa, m’dzikoli muli abale ndi alongo 640 amene amalankhula Chiesani komanso muli mipingo ya chinenerochi yokwana 10.
Baibulo la Malemba Achigiriki ndi loyamba kumasuliridwa m’Chiesani. Baibuloli lisanatulutsidwe, abale ndi alongo oyankhula Chiesani ankagwiritsa ntchito Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chingelezi. Pofotokoza za mawu akuti “tili ndi chuma chimenechi mʼziwiya zadothi” omwe akupezeka pa 2 Akorinto 4:7, mlongo wina ananena kuti: “Ndikukumbukira nthawi imene ndinawerenga vesi limeneli m’Chingelezi koma sindinamvetse tanthauzo lake. Koma Baibulo la Dziko Latsopano la Chiesani linamasulira kuti: ‘Ngakhale kuti tili ngati ziwiya zadothi, Mulungu anatipatsa utumiki wamtengo wapatali.’ Panopa sindikuvutikanso kumvetsa mfundo yake ndipo ikundifika pamtima. Baibuloli ndi mphatso yamtengo wapatali!”
Tikusangalala limodzi ndi abale athu oyankhula Chiedo komanso Chiesani chifukwa cha kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu m’zinenero ziwirizi ndipo ndi pemphero lathu kuti Mabaibulowa athandizenso anthu ena ‘kudziwa choonadi molondola.’—1 Timoteyo 2:3, 4.