Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 23, 2018
NIGERIA

Mvula Yamphamvu Yachititsa Kuti Madzi Asefukire Kwambiri ku Nigeria

Mvula Yamphamvu Yachititsa Kuti Madzi Asefukire Kwambiri ku Nigeria

Mvula yamphamvu yomwe inagwa m’dziko la Nigeria inachititsa kuti madzi asefukire kwambiri m’chigawo chapakati ndiponso kum’mwera kwa dzikolo. Madziwa anasefukira kwambiri m’mitsinje ikuluikulu ya dzikolo, mtsinje wa Benue ndi Niger. Madzi osefukirawo anapha anthu oposa 100 ndipo enanso masauzande ambiri akusowa pokhala.

Malipoti oyambirira akusonyeza kuti palibe wa Mboni amene wafa kapena kuvulala. Komabe, ofalitsa osachepera 2,000 akusowa pokhala ndipo ofalitsa oposa 1,000 pa ofalitsawa akufunikira chithandizo. Ambiri mwa ofalitsa amene anathawa m’nyumba zawo akusungidwa ndi a Mboni anzawo omwe ali m’madera omwe sanakhudzidwe ndi madzi osefukirawo.

Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi yakhazikitsidwa kuti iyendetse ntchito yopereka chithandizo komanso kulimbikitsa abale awo ndi mfundo za m’Baibulo. Kuwonjezera pamenepa, abale awiri a m’Komiti ya Nthambi ya ku Nigeria limodzi ndi woyang’anira dera ndi abale omwe amatumikira mu Dipatimenti ya Utumiki ndi Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga, anakayendera ofalitsa okhala m’madera omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi kuti akawalimbikitse.

Ngakhale kuti abale athu akumana ndi mavuto ambiri chifukwa cha ngoziyi, Yehova Atate wathu wakumwamba akupitirizabe kukhala “malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya nsautso.”—Salimo 37:39.