NOVEMBER 18, 2019
NORTH MACEDONIA
‘Kuwolokera ku Makedoniya’ Kukagwira Nawo Ntchito Yapadera Yolalikira
Ofesi ya nthambi ya North Macedonia inakonza ntchito yapadera yolalikira kuyambira pa 1 August mpaka pa 31 October, 2019. Ntchitoyi inakonzedwa n’cholinga cholalikira kwa anthu a m’gawo la nthambiyi omwe amayankhula Chimakedonia ndi Chiabeniya.
Ku North Macedonia kuli anthu oposa 1.3 miliyoni omwe amayankhula Chimakedonia ndiponso anthu opitirira 500,000 omwe amayankhula Chiabeniya. Komabe, pa ofalitsa 1,300 a m’dzikoli pali ofalitsa pafupifupi 1,000 omwe ali m’gawo loyankhula Chimakedoniya ndipo ofalitsa 20 okha ndi amene amathandiza m’gawo la Chiabeniya. Pofuna kuthandiza ofalitsawa, abale ndi alongo okwana 476 ochokera m’mayiko 7 anapita ku North Macedonia kuti akagwire nawo ntchitoyi. Iwo anachokera m’mayiko otsatirawa: Albania, Austria, Belgium, Germany, Italy, Sweden, ndi Switzerland.
Pa nthawi yomwe abalewa ankalalikira, m’bale wina anakumana ndi munthu yemwe amagwira ntchito yoweta mbuzi. Munthuyo atazindikira kuti akuyankhula ndi wa Mboni za Yehova, anapisa m’chikwama chake ndi kuonetsa m’baleyo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Iye anauza m’baleyo kuti analandira bukulo kwa a Mboni ochokera ku Italy omwe anadzagwiranso ntchito yolalikira yapadera zaka 10 zapitazo. Munthuyo ananenanso kuti amawerenga buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani tsiku lililonse ndipo analoweza mitu ina. Abalewa anakonza zoti adzamuyenderenso.
Zimene abale oyankhula Chimakedoniya ndi Chiabeniya anachita podzipereka ndi mtima wonse kugwira nawo ntchitoyi, zikutikumbutsa zimenenso Paulo anachita povomera ndi mtima wonse atapemphedwa kuti: “Wolokerani ku Makedoniya kuno.”—Machitidwe 16:9.