Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni Ku Palestinian Territory
Kuyambira mu 1919, a Mboni za Yehova akhala akupezeka m’chigawo chimene panopa chimadziwika kuti Palestinian Territory. Mu 1920, iwo anakhazikitsa mpingo mumzinda wa Ramallah ndipo anadzakhazikitsanso mpingo wachiwiri pafupi ndi tawuni ya Betelehemu mu 1942. Nkhondo yomwe inachitika ku Palesitina mu 1948 inachititsa kuti derali ligawidwe m’zigawo ziwiri. Chigawo choyamba chinakhala dziko la lsrael wamasiku ano ndipo chigawo china chinayamba kulamuliridwa ndi dziko la Jordan. Kwa zaka pafupifupi 20 a Mboni a ku Israel ndi a ku Palestinian Territory sankatha kulumikizana. Mu 1967, pambuyo pa nkhondo yomwe inatenga masiku 6, anayambiranso kulumikizana ndipo anayambanso kusangalala ndi ufulu wosonkhana komanso wochitira zinthu limodzi ku West Bank.
Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ku Palestinian Territory akhala akupempha kulembetsa chipembedzo chawo kuti chikhale chovomerezeka ndi boma, akuluakulu a boma amawakanira. A Mboni amatha kusonkhana pamodzi n’kumalambira Mulungu komanso amalalikira kwa anthu, koma chifukwa choti sanalembetsedwe ku boma, sapatsidwa ufulu womwe anthu ena ali nawo. Panopa akuyesetsa kuti apatsidwe maufulu ndiponso kuti alembetse chipembedzo chawo kuti chikhale chovomerezeka ndi boma.