Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 2, 2016
DERA LA PALESTINA

A Mboni za Yehova Akuvutika Kuti Apatsidwe Ufulu Wonse Kudera la Mapalestina

A Mboni za Yehova Akuvutika Kuti Apatsidwe Ufulu Wonse Kudera la Mapalestina

Mike Jalal ndi Natali Sa’ad ndi a Mboni za Yehova ku Palestina ndipo anakwatirana mwalamulo koma boma siliwalola kuti adule mtchatho. Posachedwapa, anapeza movutikira kwambiri kalata yosonyeza tsiku lobadwa la mwana wawo wamng’ono dzina lake Andrae. Koma sikuti ndi banja lawo lokha limene likuvutika chonchi. Nawonso a Mboni ena akukumana ndi vuto lomweli. Popeza kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova sichinalembedwe m’kaundula wa ku Palestina, a Mboniwo amalephera kuchita zinthu zina.

Alibe Ufulu Chifukwa Choti Chipembedzo Chawo Sichinalembedwe M’kaundula wa Boma

A Sa’ad anakwatirana ali ku Israel ndipo amene anakwatitsa ukwati wawo ndi m’busa wina wa Mboni za Yehova. Koma Unduna Woona za M’dziko ku Palestina unakana kulemba ukwati wawo m’kaundula chifukwa chakuti chipembedzo chawo cha Mboni za Yehova sichinalembedwe m’kaundula wa m’dzikoli. Popeza kuti a Sa’ad sakuloledwa kuti alembetse ukwati wawo, poyamba undunawu unkakananso kuti ulembe mwana wawo m’kaundula. Banja la a Sa’ad ndiponso a Mboni ena akhala akuyesetsa kupempha boma kuti liwalole kulembetsa ana awo m’kaundula.

Boma Linavomera Kupereka kwa Ana a Mboni Makalata Osonyeza Tsiku lawo Lobadwa

Mu 2014, Unduna Woona za M’dziko ku Palestina unalola kuti a Mboniwo alembetse ana awo m’kaundula wa dzikolo. Banja la a Sa’ad likusangalala kuti panopa mwana wawo, yemwe anabadwa pa 30 January 2012, wapeza kalata yosonyeza tsiku lake lobadwa. Makolo a Maya Jasmin, a Laura, ndiponso a Cristian, omwe ali pachithunzi cham’mwambacho, akuyamikiranso kuti undunawo wapereka kwa ana awo makalata osonyeza masiku awo obadwa komanso osonyeza kuti anawo ndi Akhristu.

Panopa anawo ali ndi ufulu umene nzika zina zimakhala nawo chifukwa chokhala ndi makalatawo. Mwachitsanzo, makolo awo akhoza kuyenda nawo kumayiko ena popanda mavuto komanso kukawalembetsa m’sukulu zam’dzikoli.

A Mboni Sakuloledwabe Kuti Adule Mtchatho

Ngakhale kuti a Mboni analoledwa kuti apeze makalatawo, boma likukanabe kuti a Sa’ad komanso mabanja ena 7 a Mboni adule mtchatho. Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amawaona molakwika kuti sali pa banja ndipo akungokhalira limodzi.

Izi zimachititsanso kuti mwamuna ndiponso mkazi m’banjamo azilipira msonkho wakewake komanso kukhala ndi akaunti yakeyake kubanki. Ngati wina atadwala kwambiri kapena kuchita ngozi, mwamuna kapena mkazi wake sangamusankhirenso zochita pa nkhani ya mankhwala. Komanso ngati wina wamwalira, mwamuna kapena mkazi wake ndiponso ana ake sangapatsidwe katundu wa womwalirayo. Akhristu sangaikenso m’manda achibale awo amene anamwalira motsatira zimene amakhulupirira. Koma amayenera kuwaika m’manda achisilamu pamalo amene amaika anthu omwe si Asilamu.

Akuyesetsa Kupempha Boma Kuti Chipembedzo Chawo Chilembedwe M’kaundula

Mu September 2010, a Mboni za Yehova anapempha boma kuti liwalole kulembetsa chipembedzo chawo m’kaundula wa boma. Koma panadutsa zaka ziwiri nkhaniyi isanayankhidwe. Choncho a Mboniwo anatumizanso kalata kukhoti lalikulu, lomwe lili mumzinda wa Ramallah, yopempha kuti aloledwe kulembetsa chipembedzo cha Mboni za Yehova m’kaundula. Koma khotili linakana zimene anapemphazo mu October 2013.

Kuchokera nthawi imeneyo, a Mboni akhala akuyesetsa kukumana ndi akuluakulu a boma kuti awathandize kuthetsa vutoli. Koma nkhaniyi sikutha chifukwa akuluakuluwo sakuchita chilichonse.

A Philip Brumley, omwe ndi loya wa Mboni za Yehova, anati: “A Mboni akhala mumzinda wa Ramallah komanso m’madera ena ozungulira mzindawu kwa zaka pafupifupi 100. Iwo amasangalala kwambiri kuti akuluakulu a boma amawalola kuti azichita zachipembedzo chawo mwaufulu. Komabe si bwino kuti a Mboni azisalidwa posaloledwa kulembetsa chipembedzo chawo m’kaundula zomwe zikuchititsa kuti asamalandire ufulu wawo wonse.”

A Mboni za Yehova akuyamikira zimene akuluakulu a boma achita powalola kuti apezere ana awo makalata osonyeza tsiku lawo lobadwa. Mabanja a Mboni omwe panopa sakuloledwa kudula mtchatho akukhulupirira kuti boma liwathandiza pa nkhaniyi komanso lilola kuti a Mboni alembetse chipembedzo chawo m’kaundula.