Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 19, 2019
PERU

A Mboni za Yehova ku Peru Awonjezera Ntchito Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri

A Mboni za Yehova ku Peru Awonjezera Ntchito Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri

Abale ndi alongo athu pafupifupi 3,000 ku Peru akugwira nawo ntchito yapadera yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri pa nthawi ya masewera a Pan American Games ndi Parapan American Games omwe akuchitikira mumzinda wa Lima. Pa masewerawa omwe anayamba pa 26 July, 2019 ndipo adzatha pa 1 September, pakhala anthu oposa 8,500 omwe achite nawo masewerawa komanso pafika alendo pafupifupi 250,000.

Pofuna kuti athe kulalikira kwa alendo omwe ndi ochuluka kwambiri, ofalitsa anaika mashelefu 100 m’malo 53 osiyanasiyana. Mashelefuwa ali ndi mabuku, magazini ndi mapepala m’zinenero za Chiayimara, Chingelezi, Chifulenchi, Chipwitikizi, Chikwechuwa (Ayacucho), ndi Chisipanishi. Alinso ndi mavidiyo a Chinenero Chamanja cha ku Peru a anthu omwe ali ndi vuto losamva.

M’bale Kemps Moran Hurtado yemwe akuthandiza kuyendetsa ntchito yolalikirayi, anati: “Ntchito yapaderayi itipatsa mwayi wolalikira kwa anthu ambiri a zikhalidwe zosiyanasiyana chifukwa ku masewerawa kumafika anthu a m’mayiko osiyanasiyana. Kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndi mbali yofunika kwambiri pa ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo. Imapereka kwa anthu mwayi wapadera woona a Mboni za Yehova akulalikira m’malo omwe mumapezeka anthu ambiri.”

Ndife osangalala kumva za kuonjezeka kwa ntchito yolalikirayi. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kudalitsa ntchito ya abale ndi alongo athu ku Peru pamene akupitiriza kulalikira kulikonse kumene anthu angapezeke.—Machitidwe 17:17.