JANUARY 29, 2019
PERU
Msonkhano Wapadera Womaliza mu 2018 Unachitikira ku Peru
A Mboni za Yehova ku Peru analandira alendo 3,400 ochokera m’maofesi a nthambi 9 omwe anapita kukachita nawo Msonkhano Wapadera womwe unali womaliza mu 2018. Msonkhanowu unali ndi mutu wakuti “Limbani Mtima,” ndipo unachitikira pa sitediyamu ya Monumental mumzinda wa Lima womwe ndi likulu la dzikolo, kuyambira pa 23 mpaka 25 November. Anthu omwe anasonkhana pa sitediyamuyi komanso omwe analumikizidwa m’madera ena, onse pamodzi anali 66,254. Komanso, abale ndi alongo atsopano okwana 719 anabatizidwa. Msonkhanowu unkachitika pa nthawi imodzi m’Chingelezi, m’Chinenero Chamanja cha ku Peru, m’Chikwechuwa (cha ku Ayacucho) ndi m’Chisipanishi.
Nthawi yapadera kwambiri inali pamene alendowo anali ndi mwayi wolowa muutumiki wakumunda limodzi ndi abale ndi alongo a m’dzikolo. Iwo anasangalalanso ndi chakudya, chikhalidwe komanso kuona malo ku ofesi ya nthambi ya ku Peru.
A Ezequiel Porras, omwe anayankhula m’malo mwa ofesi ya nthambi ku Peru anati: “Msonkhano wapaderawu wakhudza anthu ambiri kuno ku Peru. Sikuti unangokhala msonkhano wosaiwalika kwa abale ndi alongo athu, koma unathandizanso kwambiri kuti anthu a m’derali atidziwe. Tikuthokoza Yehova chifukwa cha mwayi wapadera umenewu wotamanda dzina lake lalikulu.”—1 Petulo 2:12.
Mu sitediyamu ya Monumental munaikidwa madamu obatizira ambirimbiri amene anagwiritsidwa ntchito pobatiza anthu 483. Anthu enanso 236 anabatizidwa m’madera omwe analumikizidwa.
Alendo ochokera ku mayiko ena analalikira limodzi ndi abale ndi alongo a m’dzikolo.
M’bale Samuel Herd wa m’Bungwe Lolamulira, ankakamba nkhani yomaliza tsiku lililonse.
Abale ndi alongo a m’dzikoli analandira alendo ndi manja awiri pamene ankafika pabwalo la ndege la Jorge Chávez International Airport ku Lima.
Pa nthawi yomwe alendo ankaona malo ku ofesi ya nthambi, anasonyezedwanso mmene dzina la Mulungu linasungidwira m’Baibulo.
Abale anasonyeza alendowa kaphikidwe ka zakudya zosiyanasiyana za ku Peru pa nthawi yomwe ankachita zinthu m’magulu pa Malo a Msonkhano. Apa akukonzera alendo chakudya chotchedwa ceviche.
Akusonyeza alendo mmene amasokera zovala zachikhalidwe. Ulusi wake amaupaka utoto wamitundu yosiyanasiyana wochokera ku zomera.
Alendo omwe ankaona malo pa ofesi ya nthambi anasangalala pa mwambo wapadera womwe unachitika madzulo ndipo panaimbidwa nyimbo yomwe uthenga wake unali wochokera mu nyimbo yakuti: “Timadzipereka.” Pamwambowu panalinso nyimbo zachikhalidwe, kuvina, komanso zida zoimbira zochokera m’zigawo zikuluzikulu za ku Peru zotchedwa coastal desert, Andes Mountains, ndi Peruvian rain forest.
Akuvina gule wachikhalidwe cha ku Trujillo madzulo.
Anasonyeza zitsanzo za ulaliki zosiyanasiyana. Nyumba ya zidina komanso zovala zomwe zikuonekazo, zikusonyeza chikhalidwe cha anthu a mtundu wa Quechua omwe amakhala m’madera a kumapiri mumzinda wa Cuzco.
Pomaliza mwambo wamadzulowu, onse omwe anali ndi mbali zosiyanasiyana akubayibitsa anthu.