OCTOBER 17, 2019
PERU
Ntchito Yapadera Yolalikira Inathandiza Anthu Oyankhula Chiayimara ku Peru
Kuyambira pa 1 May mpaka pa 31 August, 2019, ofesi ya nthambi ya Peru inakonza ntchito yapadera yolalikira pofuna kuthandiza anthu omwe chinenero chawo chobadwira ndi Chiayimara, kuti amve uthenga wa m’Baibulo. Ntchitoyi inayenda bwino kwambiri. Abale ndi alongo anagawira mabuku ndi zinthu zina zoposa 7,893 komanso anaonetsa anthu mavidiyo maulendo 2,500. Pamene ntchitoyi inkatha, abale athuwa anali atayambitsa maphunziro a Baibulo 381.
Anthu pafupifupi 450,000 ku Peru amalankhula Chiayimara ndipo mwa anthuwa, pafupifupi 300,000, amakhala m’chigawo cha Puno. Panopa, kuli ofalitsa 331 olankhula Chiayimara ndipo amasonkhana m’mipingo 7 ndi m’magulu 8. Chifukwa choti gawoli ndi lalikulu kwambiri poyerekezera ndi chiwerengero cha ofalitsa a m’dziko la Peru, ofalitsa ochokera m’dziko la Chile omwe amalankhula Chiayimara anathandiza nawo pa ntchito yapaderayi. Pofuna kulalikira anthu olankhula Chiayimara omwe amakhala m’madera akumapiri, nthawi zina abale athuwa ankakwera mtunda wautali mamita 5,000 ndipo ankalalikira kukuzizira kwambiri (0ºC).
Gulu lina la abale ndi alongo linayenda kwa maola ambiri kupita m’dera lina lomwe anthu ochokera m’tawuni ina yapafupi anasonkhana pamwambo wa maliro. Abale ndi alongowa analalikira kwa anthuwo uthenga wa m’Baibulo wokhudza chiyembekezo cha anthu omwe anamwalira. Akuluakulu a m’deralo komanso anamfedwa anayamikira abale ndi alongowa chifukwa chowauza uthenga wotonthoza wa m’Baibulo.
M’dera lina, abale ndi alongo athuwa anapeza gulu la anthu ena omwe ankasonkhana kawiri pa mlungu kuti aziphunzira Baibulo. Abalewa anazindikira kuti anthuwa ankaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako komanso Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ndipo wachibale wawo yemwe ankakhala ku Bolivia ndi amene anawapatsa mabukuwa. Anthuwo atangodziwa kuti gulu lathu ndi limene linafalitsa mabukuwa, ambiri anayamba kuphunzira Baibulo ndi abalewa ndiponso kupezeka pamisonkhano yathu.
M’bale Albert Condor, yemwe ndi mkulu mumpingo ndiponso anatsogolera gulu lina la abale ndi alongo, anati: “Ine ndi mkazi wanga tikusangalala kwambiri chifukwa choti tagwira nawo ntchito yapaderayi. Zimenezi zatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova chifukwa pa nthawi yomwe tinkanyamuka kupita kutawuniyi, sitinkadziwa bwinobwino kuti tikafikako bwanji popeza kuti ulendowu unali wovuta. Titangofika, tinapemphera kwa Yehova kuti atithandize kupeza malo okhala. Yehova anatiyankha. Mapemphero omwe tinapereka anandilimbitsa kwambiri. Chikhulupiriro changa chinalimbanso kwambiri nditaona kuti abale ena amadalira kwambiri Yehova.”
Abale ndi alongowa akusangalala kugwira nawo ntchito yothandiza anthu a mumzinda wa Puno ku Peru omwe amalankhula Chiayimara. Ntchitoyi ikuthandiza anthuwa kupeza choonadi cha m’Mawu a Mulungu chomwe chidzawathandize kupeza moyo wosatha.—Chivumbulutso 22:17.