Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 3, 2019
PHILIPPINES

A Mboni za Yehova ku Philippines Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano M’zinenero Zitatu

A Mboni za Yehova ku Philippines Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano M’zinenero Zitatu

Pamisonkhano yapadera yomwe inachitika mu January 2019, M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira, anatulutsa Baibulo m’Chisebuwano, m’Chitagalogi ndi m’Chiwarayiwarayi. Baibulo la Chisebuwano linatulutsidwa pa 12 January ku Hoops Dome, mumzinda wa Lapu-Lapu. Tsiku lotsatira Baibulo la Chiwarayiwarayi linagawidwa pa Leyte Academic Center ku Palo, m’chigawo cha Leyte. Pa 20 January, Baibulo la Chitagalogi linatulutsidwa ku Malo a Msonkhano a Metro Manila mumzinda wa Quezon.

Banja likusangalala pambuyo polandira Baibulo la Dziko Latsopano la Chisebuwano lokonzedwanso.

Nyumba za Ufumu zambirimbiri zinalumikizidwa ku misonkhanoyi ndipo Mabaibulo a Dziko Latsopano opitirira 163,000 anagawidwa.

M’bale Dean Jacek, wa ku ofesi ya nthambi ya ku Philippines anati: “Mabaibulo a Dziko Latsopano omwe atulutsidwa mu Chisebuwano ndi Chitagalogi ndi okonzedwanso ndipo panatenga zaka zoposa zitatu kuti lililonse limalizidwe. Poyamba Baibulo la Chiwarayiwarayi linalipo la Malemba Achigiriki lokha, choncho aka kakhala koyamba kuti anthu akhale ndi Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu. Ntchito yomasulira Baibuloli inatenga zaka zoposa 5.”

M’dziko la Philippines, anthu oposa 60 pa 100 alionse amalankhula Chisebuwano, Chitagalogi, kapena Chiwarayiwarayi. Anthuwa akuphatikizapo abale ndi alongo athu pafupifupi 160,000 komanso ophunzira Baibulo oposa 197,000. Palinso anthu ambirimbiri a ku Philippines amene akukhala m’mayiko ena omwe panopa atha kusangalala ndi zinthu zosiyanasiyana zothandiza pophunzira zomwe zili m’Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenerozi.

Mlongo Donica Jansuy yemwe amasonkhana mumpingo wa Chitagalogi ku United States, atapanga dawunilodi Baibulo lake latsopano ananena mawu otsatirawa: “Mawu omwe ali mu Baibulo la Chitagalogi lokonzedwanso ndi osavuta komanso omveka bwino, ndipo zimenezi zikuchititsa kuti likhale losavuta kumva. Mawu osavuta omwe anagwiritsidwa ntchito m’Baibuloli akutipangitsa kumva ngati Yehova akuyankhula nafe wina aliyense payekha, ndipo zimenezi zikuchititsa kuti uthenga wa m’Baibulo uzitifika pamtima mosavuta.”

Pofika pano, a Mboni za Yehova amasulira mbali zina za Baibulo la Dziko Latsopano kapena lonse lathunthu m’zinenero 179. Tikuthokoza Yehova pothandiza kuti abale ndi alongo athu komanso anthu amene amawauza uthenga wa m’Baibulo, akhale ndi Mabaibulo omasuliridwa momveka bwino.—Machitidwe 13:48.