Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 13, 2019
PHILIPPINES

Mphepo Yamkuntho Inawononga M’madera Ena ku Philippines

Mphepo Yamkuntho Inawononga M’madera Ena ku Philippines

Mphepo Yamkuntho ya Kammuri yomwe imadziwikanso kuti Tisoy ku Philippines inawomba pa 2 December, 2019, m’chigawo cha kum’mwera kwa chilumba cha Luzon. Ngakhale kuti palibe wa Mboni za Yehova aliyense yemwe anafa kapena kuvulala, nyumba 108 za mabanja a Mboni zinawonongeka kwambiri ndipo zina 478 zinaonongeka pang’ono. Komanso, Nyumba za Ufumu 15 zinaonongeka.

Popeza kuti mphepo yamkunthoyi inawononga zinthu m’dera lalikulu, ofesi ya nthambi ya Philippines inakhazikitsa makomiti 8 kuti athandize abale ndi alongo powalimbikitsa komanso kuwapatsa thandizo la ndalama ndi zinthu zina.

Tikupempherera abale athu ku Philippines ndipo mofanana ndi wamasalimo tikunena kuti: “Yehova akuyankheni pa tsiku la nsautso. . . . Atumize thandizo kuchokera kumalo oyera.”—Salimo 20:1, 2.