Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Nyumba ziwiri mwa nyumba zitatu za a Mboni zomwe zinawonongeka kwambiri ndi mphepo yamkunthoyi.

JANUARY 22, 2019
PHILIPPINES

Mphepo Yamkuntho Yawononga Kwambiri Kum’mawa Kwa Philippines

Mphepo Yamkuntho Yawononga Kwambiri Kum’mawa Kwa Philippines

Pa 29 December, 2018, mphepo yamkuntho yotchedwa Usman inaomba pa chilumba cha Samar, chomwe ndi chilumba chachitatu pazilumba zikuluzikulu za ku Philippines. Mphepoyi inabweranso ndi mvula yamphamvu kwambiri yomwe inachititsa kuti nthaka ikokoloke komanso madzi asefukire. Anthu osachepera 25 anafa, 42 anavulala ndipo nyumba 22,835 zinaonongeka.

Ofesi ya nthambi ya ku Philippines yanena kuti palibe m’bale kapena mlongo amene wafa ndi mphepo yamkunthoyi. Komabe, nyumba zitatu za abale athu zinawonongekeratu, ndipo nyumba 4 zinawonongeka pang’ono. Kuonjezera pamenepo, Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka. Motsogoleredwa ndi ofesi ya nthambi, Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi inapereka zinthu zofunika komanso nyumba zongoyembekezera kwa mabanja omwe anakhudzidwa.

Tikukhulupirira kuti abale ndi alongo athu omwe anakhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyi apitiriza kudalira Yehova, podziwa kuti awalimbitsa komanso awapatsa mphamvu.—1 Petulo 5:10.