6 OCTOBER, 2022
PHILIPPINES
Mphepo Yamkuntho ya Noru Yawononga ku Philippines
Pa 25 September 2022, mphepo yamkuntho ya Noru yomwe anthu a m’dziko la Philippines amaitchulanso kuti Karding, inawomba pazilumba za Polillo m’chigawo cha Quezon. Pambuyo pake, mphepoyi inawombanso m’chigawo cha Aurora. Mphepoyi imathamanga pa liwilo la makilomita 195 pa ola limodzi. Mphepo yamkuntho ya Noru inawononga nyumba zambiri, misewu ndi mabuliji komanso inachititsa kuti madzi anasefukira dera lalikulu.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi
Mabanja 180 anasamuka m’nyumba zawo
Nyumba 209 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 20 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 22 zinawonongekeratu
Nyumba za Ufumu 7 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri
Ntchito Yopereka Chithandizo
Panakhazikitsidwa Makomiti Othandiza Pangozi Zamwadzidzidzi okwana awiri
Akulu a m’deralo akulimbikitsa mwauzimu mabanja okhudzidwa komanso kuwapatsa zinthu zofunikira
Ntchito zonse zopereka chithandizo, zikugwiridwa potsatira njira zodzitetezera ku COVID-19
Tipitirizabe kupempherera abale athu omwe akhudzidwa ndi mphepoyi pomwe akudalira Yehova kuti awateteze.—Salimo 57:1.