Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 2, 2020
PHILIPPINES

Mphepo Yamkuntho ya Phanfone Yawononga ku Philippines

Mphepo Yamkuntho ya Phanfone Yawononga ku Philippines

Pa 24 December, 2019, mphepo Yamkuntho ya Phanfone yomwe imadziwikanso kuti Ursula inaomba m’chigawo cha Eastern Samar ku Philippines. Palibe wa Mboni aliyense yemwe anafa kapena kuvulala. Komabe, nyumba 464 za a Mboni zinawonongeka kuphatikizaponso Nyumba za Ufumu 6. Ofesi ya nthambi ya Philippines yakhazikitsa makomiti 5 kuti alimbikitse komanso kupereka chithandizo kwa abale ndi alongo omwe amakhala m’madera omwe anakhudzidwa ndi mphepoyi.

Mphepo ya Phanfone ndi ya nambala 21 pa mphepo zamkuntho zomwe zinaomba ku Philippines mu 2019. Komanso posachedwapa kunachitika zivomezi zomwe zinawononga kum’mwera kwa dzikoli. Chifukwa cha zimenezi, panopa kuli makomiti 18 omwe akuthandiza abale ndi alongo okhudzidwa ndi ngozi zimenezi.

Tikuthokoza kwambiri abale athu a ku Philippines chifukwa choti akupitirizabe kupirira ndiponso kudalira Yehova yemwe ndi Mulungu “wachikondi chachikulu ndi wachifundo.”—Yakobo 5:11.