22 DECEMBER, 2021
PHILIPPINES
Mphepo Yamkuntho ya Rai Yawononga ku Philippines
Mkuntho wa Rai (anthu a m’dzikoli amautchulanso kuti Odette) unafika m’madera ambiri a m’dziko la Philippines kuyambira pa 16 mpaka pa 18 December, 2021. Mkunthowu utawomba kwa nthawi yoyamba pachilumba cha Siargao, unkathamanga pa liwiro la makilomita 195 pa ola limodzi. Mkunthowu unawononga kwambiri madera ngati Northern Mindanao, Southern Luzon komanso Visayas.
Mmene Zinakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Zomvetsa chisoni kuti ofalitsa 4 anafa
Wofalitsa mmodzi sakupezekabe
Abale ndi alongo 12 anavulala
Ofalitsa oposa 2,000 anakakamizika kusamuka m’nyumba zawo
Nyumba 246 zinawonongekeratu
Nyumba 327 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 1,174 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu 43 zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Ma Komiti Othandiza pa Ngozi Zamwadzidzidzi okwanira 6 anakhazikitsidwa kuti ayang’anire ntchito yopereka chithandizo
Akulu a m’madera okhudzidwa analimbikitsa abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi tsokali kuphatikizaponso amene anaferedwa
Ntchito zonse zopereka chithandizo, zikugwiridwa potsatira njira zodzitetezera ku COVID-19
Motsogoleredwa ndi akulu, abale ndi alongo am’madera ena, anapereka chakudya ndi zovala kuti zikathandize ofalitsa a m’madera omwe anakhudzidwa ndi tsokali. Mwamsanga abale ndi alongo a mumzinda wa Davao anapereka chakudya kuti chikathandize mabanja omwe ankafunikira thandizo mumzinda wa Surigao.
Tili ndi chisoni kuti abale ndi alongo athu ena okondedwa anafa pa tsokali. Pomwe tikulimbana ndi mavuto a ‘m’nthawi yapadera komanso yovutayi,’ tipitirizabe kudalira Yehova kuti atithandize ndi kutitonthoza.—2 Timoteyo 3:1.