Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere: Nyumba ya Ufumu yomwe inawonongekeratu ndi mphepo yamkuntho. Kumanja: Mapu osonyeza dera limene linakhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyi

MAY 28, 2020
PHILIPPINES

Mphepo Yamkuntho ya Vongfong Yawononga ku Philippines Pamene Nyengo Yamvula Ikuyamba

Mphepo Yamkuntho ya Vongfong Yawononga ku Philippines Pamene Nyengo Yamvula Ikuyamba

Pa 14 May 2020, mphepo yamkuntho ya Vongfong (yomwenso imadziwika kuti Ambo) inawomba pachilumba cha Samar. Aka ndi koyamba m’chaka cha 2020 kuti kumadzulo kwa Nyanja ya Pacific kuwombe mphepo yamphamvu kwambiri chonchi. Mphepoyi inawononga pachilumba cha Samar ndipo inkawomba paliwiro la makilomita 185 pa ola. Anthu masauzande ambiri anathawa m’nyumba zawo. Kuchita zimenezi kunali kovuta chifukwa choti boma linali litauza anthu kuti azikhala motalikirana.

Ngakhale kuti palibe m’bale kapena mlongo aliyense yemwe anavulala, abale ndi alongo 59 anathawa m’nyumba zawo. Abale ena anakakhala m’masukulu omwe akugwiritsidwa ntchito ngati malo ogona pamene ena anakakhala nawo m’nyumba za abale ndi alongo anzawo. Nyumba 82 zinagweratu pamene zina mwa nyumbazi zinangowonongeka. Komanso Nyumba za Ufumu 5 zinawonongeka ndipo imodzi inawonongekeratu. Komiti ya Ofesi ya Nthambi ya Philippines inakhazikitsa makomiti awiri opereka chithandizo pakagwa mavuto a mwadzidzidzi kuti asamalire abale ndi alongo omwe anakhudzidwa komanso kuwathandiza kulimbitsa chikhulupiriro chawo.

Tipitirizabe kupempherera abale athu ku Philippines omwe akuvutika chifukwa cha mphepo yamkuntho komanso mliri woopsa pa nthawi imodzi. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova, yemwe ndi “Thanthwe mpaka kalekale” apitiriza kuwasamalira powapatsa zinthu zofunikira.—Yesaya 26:4.