Pitani ku nkhani yake

AUGUST 5, 2019
PHILIPPINES

Zivomezi Zamphamvu Zagwedeza ku Philippines

Zivomezi Zamphamvu Zagwedeza ku Philippines

Pa 27 July, 2019, zivomezi ziwiri zinaononga kwambiri pachilumba chaching’ono cha Itbayat, chomwe chili pamtunda wamakilomita pafupifupi 690 kumpoto kwa mzinda wa Manila ku Philippines. Zivomezizi zinali zamphamvu, ndipo zinapha anthu 9, zinavulaza anthu 64, komanso zinaononga nyumba 266. Malipoti ochokera ku boma akusonyeza kuti anthu 2,968 anakhudzidwa ndi zivomezizi.

Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa chifukwa cha zivomezizi. Komabe, mlongo mmodzi anavulala pang’ono ndipo nyumba ziwiri za abale athu zinaonongeka kwambiri.

Ofesi ya nthambi inakhazikitsa Komiti Yothandiza Pangozi Zadzidzidzi ndiponso ikutsogolera ntchito yogula komanso kugawa zinthu zofunika monga chakudya ndi madzi. Abale oimira ofesi ya nthambi adzapita kukayendera abale ndi alongo okhudzidwa ndi ngoziyi kuti akawalimbikitse ndi mfundo za m’Baibulo komanso kukapereka zinthu zofunika.

Tikupempherera abale omwe akhudzidwa ndi zivomezi zomwe zachitika posachedwapazi. Tikudziwa kuti Yehova yemwe “ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” apitiriza kupatsa abale athuwa zinthu zofunika.—2 Akorinto 1:3.