Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Imodzi mwa nyumba 195 za abale athu zomwe zaonongeka kwambiri

NOVEMBER 18, 2019
PHILIPPINES

Zivomezi Zingapo Zawononga Kum’mwera kwa Dziko la Philippines

Zivomezi Zingapo Zawononga Kum’mwera kwa Dziko la Philippines

Zivomezi zamphamvu kwambiri zingapo zagwedeza kum’mwera kwa dziko la Philippines kuyambira pa 16 October, 2019. Anthu 21 afa, oposa 400 avulala, komanso anthu oposa 35,000 athawa m’nyumba zawo. Zivomezi zosachepera zitatu zinali zamphamvu zoposa 6.0. Zivomezi zina zing’onozing’ono zikuchitikabe m’chigawochi. Palibe m’bale wathu aliyense yemwe anafa ngakhale kuti mlongo mmodzi anavulala pang’ono.

Nyumba za Ufumu 4 komanso nyumba 195 za abale athu zinaonongeka kwambiri ndipo Nyumba za Ufumu 9 ndi nyumba 351 za abale zinaonongeka pang’ono. Abale athu ambiri akukhala m’matenti chifukwa choti ndi zoopsa kukhalabe m’nyumba zawo.

Ofesi ya nthambi ya Philippines yakhazikitsa Makomiti Othandiza Pangozi Zogwa Mwadzidzidzi awiri kuti ayendetse ntchito yothandiza anthu. Abale 6 oimira ofesi ya nthambi kuphatikizapo atatu a m’Komiti ya Nthambi anapita m’dera limene lakhudzidwa ndi zivomezizi kuti akalimbikitse komanso kutonthoza abale ndi alongo pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Tikupemphera kuti Yehova apitirize kuthandiza abale athu omwe akhudzidwa ndi zivomezizi.—Salimo 70:5.