Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 12, 2018
PHILIPPINES

Mphepo Yamkuntho ya Yutu Ikupitiriza Kuwononga ku Philippines

Mphepo Yamkuntho ya Yutu Ikupitiriza Kuwononga ku Philippines

Mphepo yamphamvu yotchedwa Yutu yomwe pa 24 October inaomba mwamphamvu kwambiri ku zilumba zakumpoto kwa Mariana, Lachiwiri pa 30 October inafikanso ku chilumba cha Luzon chomwe ndi chachikulu kwambiri ku Philippines. Mvula yamphamvu kwambiri inachititsa kuti madzi asefukire komanso nthaka inagumuka n’kupha anthu. Anthu masauzande ambiri anasamutsidwa ndipo anthu 11 anafa.

Ofesi ya nthambi ya ku Philippines inanena kuti palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anaphedwa kapena kuvulala ndi mphepoyi. Komabe, nyumba 73 za abale athu komanso Nyumba za Ufumu 6 zinawonongeka. Ofesi ya nthambi ya ku Philippines ndi imene ikuyendetsa ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa.

Tikupitiriza kupempherera abale ndi alongo athu ku Philippines omwe akhudzidwa ndi mphepo zamkuntho 18 chaka chino. Ife limodzi ndi iwowo tikudalira Yehova chifukwa tikudziwa kuti adzatichirikiza.—Salimo 55:22.