Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 14, 2013
PHILIPPINES

Mvula Yoopsa Yamkuntho, Yotchedwa Haiyan Yasakaza Zinthu Kwambiri M’dera Lapakati ku Philippines

Mvula Yoopsa Yamkuntho, Yotchedwa Haiyan Yasakaza Zinthu Kwambiri M’dera Lapakati ku Philippines

MANILA, Philippines—Pa 8 November, 2013, mvula yoopsa yamkuntho yotchedwa Haiyan (yomwe ku Philippines amaitchula kuti Yolanda) inasakaza kwambiri zinthu ku Philippines. Mvula yamkunthoyi inali yoyamba kukokolola zinthu kwambiri ku Philippines pa mvula zamkuntho zonse zimene zakhala zikuchitika m’dzikoli.

Pomafika pa November 13, 2013, Anthu a ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Philippines yomwe ili ku Manila, anapereka lipoti lakuti anthu 27 a Mboni za Yehova anamwalira chifukwa cha mvula yamkuthoyi. Ananenanso kuti nyumba zoposa 100 za anthu a Mboni komanso malo 5 ochitira misonkhano anawonongeka.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, lomwe likulu lake la padziko lonse lili ku Brooklyn, New York, likuyang’anira ntchito yopereka thandizo kwa anthu amene akhudzidwa ndi tsokali. Pa ntchito yothandiza anthuyi, Anthu a ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Philippines akhala akutumiza zakudya, madzi, mankhwala ndi zinthu zina ku madera okhudzidwa ndi mvulayi. Pofika Lamlungu pa November 10, magalimoto ang’onoang’ono okwana 10 amene ananyamula zinthu zisiyanasiyana anatumizidwa kumalowa ndipo tsiku lotsatira magalimoto ena akuluakulu anatumizidwanso.

Pa October 15, 2013, m’dera lomwe kunagwa Mvula yamkutholi munachitika chivomerezi choopsa ndipo chinapha anthu 218. Malipoti amasonyeza kuti chivomerezichi chinapha anthu atatu a Mboni za Yehova, m’modzi anafa nthaka itatembenuzika ndipo ena awiri nyumba zawo zinawagwera. Masiku atatu chivomerezichi chisanachitike, Mvula ya mkuntho yotchedwa Nari yomwe inagwa pa October 12, 2013, inapha anthu pafupifupi 13 m’dzikoli.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limayendetsa ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi masoka achilengedwe pogwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka. Anthuwa amapereka ndalamazi mwa kufuna kwawo pofuna kuthandiza pa ntchito yolalikira. Bungwe Lolamulira limapezanso anthu a maluso osiyanasiyana ndipo anthuwa amagwira ntchito mogwirizana ndi anthu odzidwa bwino ntchito a m’maofesi awo padziko lonse pothandiza anthu okhudzidwa ndi masoka achilengedwe. Amagwiranso mogwirizana ndi akuluakulu a boma a kumalo okhudzidwa ndi tsokalo limodzi ndi makomiti ena othandiza anthu okhudzidwa ndi masoka.

Bambo Dean Jacek, omwe ndi olankhulira Mboni za Yehova ku Philippines ananena kuti: “Tonse ndife achisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya anthu omwe afa patsokali. Anthu amene achibale awo amwalira komanso amene akhudzidwa mwa njira zina ndi tsokali akufunika kulimbikitsidwa kwambiri. Tipitiriza kuchita zonse zimene tingathe popereka zinthu zofunikira komanso kulimbikitsa anzathu ndi uthenga wa m’Baibulo.”

Mungalankhule ndi:

Kuchokera ku Mayiko ena lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Philippines: Dean Jacek, tel. +63 2 411 6090