Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 1, 2016
PHILIPPINES

A Mboni za Yehova Anapereka Chithandizo kwa Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Mvula Yamkuntho ku Philippines

A Mboni za Yehova Anapereka Chithandizo kwa Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Mvula Yamkuntho ku Philippines

A Mboni za Yehova akuthandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena omwe anakhudzidwa ndi mvula yamkuntho yotchedwa Typhoon Sarika (yomwe imadziwikanso ndi dzina lakuti Karen) komanso Typhoon Haima (yomwe imadziwikanso ndi dzina lakuti Lawin). Mvula yamkunthoyi inachitika kumpoto kwa chilumba cha Luzon ku Philippines, pa 16 ndi pa 19 October, 2016. Mvula ya Typhoon Haima, ili m’gulu la nambala 4 la mvula zamkuntho za mphamvu kwambiri. Mvulayi ndi imodzi mwa mvula za mphamvu zomwe zinachitika ku Philippines chichitikireni mvula yoopsa kwambiri ya Super Typhoon Haiyan yomwe inachitika mu 2013. Super Typhoon Haiyan imadziwikanso ndi dzina lakuti Yolanda.

Ku Philippines kuli a Mboni za Yehova 200,000 ndipo palibe ngakhale mmodzi yemwe anavulala kwambiri kapena kuphedwa ndi ngoziyi. Malipoti akusonyeza kuti mvula yamkuntho ya Typhoon Haima inachititsa kuti kukhale mphepo ya mphamvu kwambiri, madzi asefukire komanso miyala ndi dothi zigumuke n’kuwononga nyumba za anthu a Mboni okwana 1,058. Inawononganso Nyumba za Ufumu zomwe ndi malo awo olambirira zokwana 43.

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Philippines inakhazikitsa komiti yopereka chithandizo mumzinda wa Tuguegarao ku Luzon. Komitiyi ndi yomwe inkalandira zinthu zothandizira anthuwa monga chakudya komanso madzi akumwa abwino ndipo ma thiraki 8 anakasiya zinthuzi m’malo omwe anakhudzidwa ndi ngoziyo. Ofesi ya nthambiyi inayamba ntchito yomanga nyumba zongoyembekezera komanso yokonza nyumba ndiponso Nyumba za Ufumu zomwe zinawonongeka.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limayendetsa ntchito yothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zachilengedwe. Bungweli limagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo pofuna kuthandiza ntchito yolalikira ya padziko lonse.

Lankhulani ndi:

Padziko Lonse: David A. Semonian, Office of Public Information, 1-718-560-5000

Philippines: Dean Jacek, 63-2-224-4444