Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JANUARY 21, 2015
PHILIPPINES

Anthu Amene Anakhudziwa ndi Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Typhoon Haiyan Tsopano Amangiridwa Nyumba

Anthu Amene Anakhudziwa ndi Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Typhoon Haiyan Tsopano Amangiridwa Nyumba

MANILA, Philippines—Mphepo yamkuntho yotchedwa Typhoon Haiyan itachitika, a Mboni za Yehova anakhazikitsa ntchito yokonza kapena kumanganso nyumba pafupifupi 750. Iwo ankafuna kuti ntchitoyi igwirike kwa chaka chimodzi.

Pa avereji, anthu 5 ankamanga nyumba kwa masiku 5.

Bambo Dean Jacek, omwe ndi mneneri wa Mboni za Yehova ku Philippines, anafotokoza kuti: “Tinakonza zoti ntchitoyi ithe pofika mwezi wa September 2014. Ntchitoyi inayambika chakumayambiriro kwa chakacho, ndipo chifukwa chakuti anthu ambiri anadzipereka kugwira nawo, mwezi wa August usanathe n’komwe tinali titaimaliza.”

Anthu a m’dzikoli komanso a m’mayiko ena anathandiza pa ntchito yomanga nyumba.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linatumiza ndalama zimene a Mboni a m’mayiko osiyanasiyana anapereka kuti zithandize pa ntchitoyi. Ofesi ya Mboni za Yehova ku Manila inakhazikitsa makomiti oti ayang’anire ntchito yomanga nyumba m’madera amene anakhudzidwa. Ntchitoyi inali yokonza kapena kumanganso nyumba 167 mumzinda wa Tacloban City, nyumba 256 mumzinda wa Ormoc City, nyumba 101 mumzinda wa Cebu City, ndi nyumba 218 mumzinda wa Roxas City. A Mboni ongodzipereka 522 a ku Philippines komanso 90 a m’mayiko ena, ndi omwe anagwira nawo ntchitoyi.

Bambo Ferdinand Martin G. Romualdez, Oimira boma la Leyte.

Bambo Ferdinand Martin G. Romualdez, omwe ndi oimira boma la Leyte, ananena kuti: “Gulu Mboni za Yehova linali bungwe loyamba pa mabungwe omwe si a boma, kugwira ntchito yomanganso nyumba za anthu okhudzidwa. . . . Ine ndi banja langa komanso anthu a m’boma lathu tikusowa chonena pa zimene a Mboniwa achita.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera M’mayiko Ena:R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Philippines: Dean Jacek, tel. +63 2 411 6090