18 MAY, 2022
POLAND
Kuyendera Ogwira Ntchito Mongodzipereka Komanso Omwe Anathawa Nkhondo ku Ukraine
Kuyambira Lamlungu pa 1 May 2022, M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limodzi ndi abale ena atatu otumikira mu Komiti ya Nthambi, anakayendera abale ndi alongo omwe anathawa ku Ukraine ndipo pano ali m’dziko la Poland. Pa ulendowu, M’bale Sanderson ndi anzakewa anacheza ndi anthu omwe anathawa kwawo komanso kuwatsimikizira kuti Bungwe Lolamulira limawakonda.
Kwa masiku 6, abalewa anayenda mtunda wa makilomita oposa 2,500 akuyendera abale ndi alongo a ku Ukraine omwe anathawira m’malo osiyanasiyana m’dziko la Poland. Malowa akuphatikizapo Malo a Misonkhano 4 komanso Nyumba za Ufumu zingapo. Iwo anakumananso ndi abale omwe akugwira ntchito mongodzipereka paboda ya Poland ndi Ukraine.
M’bale wina wa ku Ukraine ananena kuti: “Ulendo umene atipangirawu watilimbikitsa kwambiri ndipo watitsitsimula ngati madzi akumwa ozizira bwino.”
Mlongo wina wa ku Ukraine ananena kuti: “Ulendowu watilimbikitsa kwambiri. Sitinayembekezere zimenezi. Tikutha kuona mmene Yehova amatikondera.”
Mlongo winanso wa ku Ukraine ananena kuti: “Mmene tinkafika ku Poland, tinalibe chilichonse. Koma tikuthokoza Yehova kuti tsopano tili ndi zonse zofunikira.”
Abalewa anakumananso ndi Akhristu ongodzipereka omwe ankagwira ntchito yothandiza anthu omwe anathawa ku Ukraine. M’bale Sanderson anawatsimikizira kuti Bungwe Lolamulira limawakonda ndipo anabwereza mawu a pa Aheberi 6:10 ndi kuwafotokozera kuti Yehova ‘sangaiwale ntchito yawo.’ Anawonjezeranso kunena kuti: “Ngakhalenso ife sitingaiwale.” Abale ongodziperekawo anafotokoza kuti amasangalala kwambiri kuthandiza Akhristu anzawo.
M’bale Vesa Väänänen wa mu Komiti ya Nthambi ya Poland ananena kuti: “Zinali zolimbikitsa kwambiri kuona mmene Yehova wasonyezera kuti akutsogolera pa chilichonse. Iye wakhala akupereka malangizo othandiza kwambiri komanso a pa nthawi yake pogwiritsa ntchito Bungwe Lolamulira komanso abale ndi alongo omwe akudzipereka kuti athandize Akhristu anzawo.”
Abale ndi alongo akupitiriza kuthandizana posatengera mmene zinthu zilili. Ndipo zimenezi zikuwathandiza kukhala osangalala chifukwa chokhala opatsa mogwirizana ndi zomwe Yesu ananena.—Machitidwe 20:35.