Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: M’bale Corneliu Cepan akukamba nkhani ya Chikumbutso m’Chiromaniya; M’bale Angelos Karamplias akumasulira nkhaniyo kwa mkaidi wolankhula Chigiriki

APRIL 20, 2021
ROMANIA

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2021—Akaidi ku Romania Anamvetsera Nkhani ya Chikumbutso Kudzera pa Vidiyokomfelensi

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2021—Akaidi ku Romania Anamvetsera Nkhani ya Chikumbutso Kudzera pa Vidiyokomfelensi

Kwa zaka 17 abale, athu akhala akukambirana Baibulo ndi akaidi a ku ndende ya Jilava Bucharest ku Romania mlungu uliwonse. Mliri wa COVID-19 utangoyamba, misonkhano yokumana pamasom’pamaso inaimitsidwa. Koma patangotsala milungu iwiri kuti mwambo wokumbukira Imfa ya Yesu uchitike pa 27 March 2021, akuluakulu oyang’anira ndende anavomera kuti misonkhanoyi izichitikabe pogwiritsa ntchito vidiyokomfelensi. Abalewa anapempha oyang’anira ndende kuti awalole kuchita mwambo wa Chikumbutso kudzera pa intaneti. Akuluakuluwo anavomera. Pamwambowu panasonkhana akaidi 21 komanso akuluakulu oyang’anira ndende 4.

M’bale Corneliu Cepan ndi amene anakamba nkhani ya Chikumbutso m’Chiromaniya. M’bale Angelos Karamplias ndi amene ankamasulira nkhaniyi m’Chigiriki kwa mkaidi wina yemwenso anali m’ndendemo. Ogwira ntchito 4 kundendeko kuphatikizapo wachiwiri kwa oyang’anira ndende anachita nawonso mwambowu.

M’bale Cepan anafotokoza kuti: “Ndimaona kuti unali mwayi wamtengo wapatali kukamba nkhani ya Chikumbutsoyi. Akaidiwa ankamvetsera mwatcheru ndipo ankaganizira za nsembe yamtengo wapatali imene Yesu anapereka chifukwa cha iwo.”

M’bale Karamplias anati: “Ndife osangalala kwambiri kuti Yehova anatsegula khomo kuti tilalikire kwa akaidiwa komanso kuti mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye uchitike. Tikuyembekezera kuti m’tsogolomu, akaidi ambiri ayamba kuphunzira Baibulo kudzera pa intaneti, n’kumalimbikitsidwa ndi Malemba.”

Tikusangalala kwambiri kuti akuluakulu oyang’anira ndende anapereka mwayi kwa akaidi kuti amvetsere nkhani ya Chikumbutso.—1 Timoteyo 2:3, 4.