Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 25, 2020
RUSSIA

A Dennis Christensen Adakali Okhulupirika Komanso Osangalala Ngakhale Kuti Akhala M’ndende Zaka Zitatu

A Dennis Christensen Adakali Okhulupirika Komanso Osangalala Ngakhale Kuti Akhala M’ndende Zaka Zitatu

Pofika pano, M’bale Dennis Christensen wakhala m’ndende kwa zaka zitatu pa zifukwa zongomunamizira. Kungochokera pamene m’baleyu anamangidwa pa 25 May, 2017, anthu ena akhala akufunsa kuti adziwe mmene zimenezi zakhudzira chikhulupiriro chake. Nthawi zonse iye amayankha kuti: “Chikhulupiriro changa chalimba kwambiri.”

M’bale Christensen akuti: “Zimene zinalembedwa m’Baibulo pa Yakobo chaputala 1 vesi 2 ndi 3, zakhala zikundichitikira. Lembali limati: ‘Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana, monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.’”

Zikuchita kuonekeratu kuti chikhulupiriro cha M’bale Christensen chalimba kwambiri ndipo chimwemwe chake chawonjezeka ngakhale pamene wakumana ndi mavuto ambiri.

Atangomangidwa, M’bale Christensen anaikidwa m’ndende yakufupi ndi kwawo mumzinda Oryol poyembekezera kuzengedwa mlandu. Patapita nthawi, mkazi wake dzina lake Irina anapatsidwa chilolezo choti akhoza kumakamuona. M’bale Christensen anakhalabe m’ndendeyo kwa zaka zoposa ziwiri mlandu wake usanazengedwe. Mu February 2019, khoti linagamula kuti M’bale Christensen akhale m’ndende zaka 6. Koma patatha miyezi itatu, khoti linakana apilo yomwe m’baleyu anapanga. Kenako anasamutsidwa kundende yomwe anali ndipo anakamuika m’ndende ina yakutali makilomita 200 kuchokera ku Oryol zomwe zinachititsa kuti atalikiranenso ndi Irina.

Kwa chaka pafupifupi chimodzi tsopano, M’bale Christensen ali ndi mwayi woti akhoza kupempha kuti atulutsidwe m’ndende nthawi yake isanakwane. Komabe atatumiza pempho lake, katatu konse sanamulole. Ngakhale zili choncho, M’bale Christensen sanakhumudwe.

M’bale Christensen ananena modzichepetsa kuti: “Ine ndi Irina siife angwiro, koma taphunzira kupirira komanso kukhalabe achimwemwe tikamakumana ndi mayesero. Komanso chofunika kwambiri n’choti zimenezi zatithandiza kuyandikira kwambiri Yehova, yemwe ndi Mulungu komanso Atate wathu.”

Tikupemphera komanso tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kuthandiza abale ndi alongo athu onse ku Russia omwe timawakonda kwambiri, kuti apitirize kupirira mwachimwemwe.—Mateyu 5:11, 12.