Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Oweruza atatu a Khoti la Mumzinda wa Oryol akulengeza chigamulo chawo chogwirizana ndi zoti m’bale Dennis Christensen akhale m’ndende kwa zaka 6

JUNE 11, 2019
RUSSIA

A Dennis Christensen Akadandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Kuti Lisinthe Chigamulo Chawo

A Dennis Christensen Akadandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Kuti Lisinthe Chigamulo Chawo

Monga mmene nkhani ina m’mbuyomu inafotokozera, pa 23  May, 2019, khoti la mumzinda wa Oryol linagwirizana ndi chigamulo choti a Dennis Christensen akhale m’ndende. Zimenezi zikutanthauza kuti M’bale Christensen afunika kukhalabe m’ndende zaka 6. Popeza kuti kwa zaka ziwiri m’baleyu wakhala akusungidwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu, zomwe ndi zofanana ndi kukhala m’ndende kwa zaka zitatu mogwirizana ndi malamulo a dziko la Russia, panopa akungofunika kukhala m’ndende zaka zitatu. Madzulo a pa 6 June, 2019, M’bale Christensen anamusamutsira kundende ina yomwe akaidi amagwirirako ntchito zakalavulagaga kuti akayambe kugwira ukaidi. M’bale Christensen akadandaula za chigamulochi ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe. Panopa anakadandaula kale ku khotili kuti ligamule kuti anachitidwa zopanda chilungamo powasunga m’ndende mlandu wawo usanazengedwe.

Tikuyamikira kwambiri M’bale Christensen chifukwa chosonyeza mzimu wodekha komanso wopirira ngakhale kuti akuchitidwabe zinthu mopanda chilungamo. Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kuthandiza m’bale Christensen komanso a Mboni za Yehova oposa 200 omwe akuimbidwa milandu ku Russia.—Salimo 27:1.

Werengani zimene m’bale Dennis Christensen analankhula M’khoti la Mumzinda wa Oryol pa 16 May, 2019.

Werengani zimene m’bale Dennis Christensen analankhula M’khoti la Mumzinda wa Oryol pa 23 May, 2019.