Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 21, 2019
RUSSIA

A Mboni za Yehova Achitiridwa Nkhanza Zoopsa Mumzinda wa Surgut ku Russia

A Mboni za Yehova Achitiridwa Nkhanza Zoopsa Mumzinda wa Surgut ku Russia

Patangopita masiku 9 kuchokera pamene khoti la ku Russia linaweruza mlandu wa a Dennis Christensen mopanda chilungamo, apolisi ofufuza milandu anachitira a Mboni za Yehova osachepera 7 nkhanza zoopsa, monga kuwagwiritsa shoko, kuwabanikitsa komanso kuwamenya. Zimenezi zinachitikira kumadzulo kwa mzinda wa Surgut ku Siberia. Pa nthawi imene ankazunza abale athuwa, apolisi ankawakakamiza kuti aulule kumene amasonkhana komanso maina a a Mboni ena.

Nkhanzazi zinayamba m’mawa pa 15 February, 2019 pamene apolisi ofufuza milandu ku Surgut anathyola n’kulowa m’nyumba za a Mboni. Pambuyo pake anamanga a Mboni ena n’kupita nawo kumaofesi awo kumene apolisiwo anayamba kuwapanikiza ndi mafunso, koma abalewa anakana kuulula zokhudza a Mboni anzawo. Ndiyeno, loya yemwe anali ku maofesiwo atachoka, abalewa ananena kuti apolisiwo anawachitira nkhanza monga: kuwaveka matumba kumutu n’kuwamata kuti asathe kupuma bwinobwino, kuwamanga nyakula, komanso kuwamenya. Apolisi atavula a Mboniwo n’kuwasiya mbulanda komanso kuwathira madzi, anawagwiritsa shoko. Zankhanzazi zinachitika kwa maola pafupifupi awiri.

Panopa a Mboni osachepera atatu adakali m’ndende. Amene atulutsidwa anapita kuchipatala kukalandira thandizo la mankhwala chifukwa choti anavulazidwa ndiponso anakadandaula za nkhaniyi kwa akuluakulu omwe angathe kuwathandiza.

Komanso pambuyo pochita chipikisheni, akuluakulu a boma la Russia anakasumira a Mboni okwana 19 ku khoti, powanamizira kuti “amachita nawo zinthu zoopsa” komanso “kutsogolera zochita za gulu loopsa.”

Nkhanza zoopsa zimene akuluakuluwa achita, n’kugwiritsa ntchito udindo wawo molakwika ndipo Malamulo a Zaupandu a boma la Russia amanena kuti ayenera kupatsidwa chilango. Ndiponso boma la Russia liyenera kumamvera malamulo omwe anakhazikitsidwa ndi mabungwe ambiri a m’mayiko ena omwe amateteza anthu kuti asamachitiridwe zankhanza. Choncho tiyesetsa kukadandaula ku makhoti a ku Russia komanso a m’mayiko ena kuti atithandize.

Kuposa zonsezi, tikudziwa kuti Yehova waona nkhanza zomwe abale athu ku Russia akukumana nazo ndipo akhala ‘thandizo lawo ndi wopereka chipulumutso.’—Salimo 70:5.