Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’mwamba (kuchokera kumanzere kupita kumanja): M’bale Boris Burylov, M’bale Aleksandr Inozemtsev

M’munsi (kuchokera kumanzere kupita kumanja): M’bale Viktor Kuchkov, M’bale Igor Turik, M’bale Yuriy Vaag

APRIL 21, 2021
RUSSIA

Abale 5 a ku Perm ku Russia, Anakhalabe Olimba Mtima Ndiponso Osangalala Asilikali Atakachita Chipikesheni M’nyumba Zawo Komanso Kuwamanga

Abale 5 a ku Perm ku Russia, Anakhalabe Olimba Mtima Ndiponso Osangalala Asilikali Atakachita Chipikesheni M’nyumba Zawo Komanso Kuwamanga

MMENE ZINTHU ZILILI PANOPA | Khoti la Russian Lagamula Kuti Abale 5 ndi Olakwa

Pa 12 May 2021, Khoti la m’boma la Perm linapereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Boris Burylov, M’bale Aleksandr Inozemtsev, M’bale Viktor Kuchkov, M’bale Igor Turik, ndi M’bale Yuriy Vaag. M’bale Turik anauzidwa kuti azitsatira malamulo enaake ali kunyumba kwa zaka 7, pomwe abale 4 enawo anauzidwa kuti azitsatira malamulowa kwa zaka ziwiri ndi hafu. Panopa abalewa sakufunika kuikidwa m’ndende.

Tsiku Lopereka Chigamulo

Khoti la m’boma la Perm posachedwapa lipereka chigamulo pa mlandu wa M’bale Boris Burylov, M’bale Aleksandr Inozemtsev, M’bale Viktor Kuchkov, M’bale Igor Turik, ndi M’bale Yuriy Vaag. a

Zokhudza Abalewa

Boris Burylov

  • Chaka chobadwa: 1941 (ku Sevastopol)

  • Mbiri yake: Anakulira m’dera la Perm. Ali ndi digiri ya zaulimi. Ali mwana mayi ake ankamuwerengera nkhani za m’Baibulo. Cha m’ma 1990, anapeza Baibulo lonse lathunthu. Mu 1996 anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova

Aleksandr Inozemtsev

  • Chaka chobadwa: 1972 (ku Kostanay)

  • Mbiri yake: Ankagwira ntchito ya usilikali. Anagwiraponso ntchito yokonza magetsi komanso yokonza magalimoto ndipo panopa akugwira ntchito yokonzanso nyumba zomwe zaonongeka. Atawerenga komanso kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, anapeza mayankho odalirika ofotokoza chifukwa chake anthufe timavutika komanso kufa. Anabatizidwa mu 1996. Anakwatira, Olesya mu 2017 ndipo akulerera limodzi mwana wawo wamkazi. Amakonda kujambula, kusewera hockey, komanso kuwedza nsomba

Viktor Kuchkov

  • Chaka chobadwa: 1967 (ku Svetlitsa)

  • Mbiri yake: Kuyambira ali mwana amakonda kusema ziboliboli. Anaphunzira ntchito yokonza komanso kuwotcherera zitsulo. Amakonda kuwedza nsomba komanso kusewera volleyball. Mu 1988 anakwatira Tanya, ndipo ali ndi mwana wamkazi. Amasangalala kwambiri kuphunzira za Mulungu. Mu 1993 anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova

Igor Turik

  • Chaka chobadwa: 1968 (ku Nelidovo)

  • Mbiri yake: Amagwira ntchito yojambula zithunzi komanso kujambula pamanja. Cha m’ma 1990, anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anasangalala kwambiri ataona kuti nkhani za m’Baibulo ndi zogwirizana. Mu 1998, anabatizidwa. Anakwatira mu 2002, ndipo panopa ali ndi mwana wamkazi komanso wamwamuna. Iye amakonda kujambula zithunzi, mavidiyo komanso kukonza mawailesi

Yuriy Vaag

  • Chaka chobadwa: 1975 (ku Lesosibirsk)

  • Mbiri yake: Anaphunzira ntchito yoyendetsa mashini okwezera zinthu m’mwamba. Amagwira ntchito yokonza magetsi komanso yazomangamanga. Pa nthawi imene ankagwira ntchito ya usilikali, mchemwali wake anamufotokozera zimene Baibulo limaphunzitsa. Ataona kuti mchemwali wakeyo wasintha makhalidwe ake chifukwa chotsatira zimene Baibulo limaphunzitsa, iye anayambanso kuphunzira Baibulo. Anabatizidwa mu 1996. Anakwatira mkazi wake Svetlana, mu 1996. Ali ndi ana awiri, wamwamuna ndi wamkazi

Milandu Yawo

Pa 17 September 2018, apolisi a gulu lachitetezo (FSB) komanso gulu lina lachitetezo anakachita chipikisheni m’nyumba zambiri mumzinda wa Perm. Anachita chipikisheni m’nyumba pafupifupi 10 za abale athu. Pa nthawi ya chipikesheniyi, akuluakulu a boma anatenga zinthu monga ndalama, mafoni komanso zipangizo zina zamakono. Viktor ndi Igor anamangidwa kwa masiku angapo ndipo kenako anakhala pa ukaidi wosachoka panyumba kwa miyezi pafupi 4. Panopa onsewa anauzidwa kuti asamachite zinthu zina, ndipo mayina awo anaikidwa pa mndandanda wa anthu amene amachita zinthu “zoopsa” ku Russia.

Aliyense wa abalewa akupitirizabe kukhala wolimba mtima komanso wosangalala ngakhale akukumana ndi mavutowa.

Yuriy anafotokoza kuti panopa amapemphera kwa Yehova nthawi zonse komanso amaganizira mozama mmene Yehova wamuthandizira. Iye anatinso: “Mawu a pa Yoswa 1:7 amandikhazika mtima pansi. Palembali ndimapezapo malangizo omwe ndiyenera kumawagwiritsa ntchito. Ndimaona kuti Yehova akuthandiza komanso kundisamalira.”

Viktor ananena kuti kuganizira mozama za gulu la Yehova kumuthandiza kuti akhalebe wodekha pa nthawi ya mlanduwu. Iye anati: “Ndinkaganizira za ukulu wa Yehova, gulu lake looneka lapadziko lapansi komanso losaoneka lakumwamba, ubale wamtengo wapatali wapadziko lonse, ntchito yolalikira imene ikuchitika padziko lonse komanso kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo. Zonsezi zinandithandiza kuti ndisamangoganizira zofuna zanga. Kenako mtima wanga unakhala m’malo.”

Igor Atabwerera kunyumba anaona kuti zinthu zina zomwe zinachitika zinali zosangalatsa. Iye ananena kuti: “Pa nthawi imene ndinali m’ndende, mwana wanga anajambula chithunzi cha dziko latsopano choti chindilimbikitse. Koma akuluakulu a kundendeko sanalole kuti mwanayo andipatse chithunzicho. Mkazi wanga anandiuza kuti, akuluakuluwo anayang’anitisitsa chithunzicho kwa kanthawi ndipo kenako anamubwezera mwanayo n’kumuuza kuti: ‘Sitingalandire chithunzi chimenechi. Imeneyi ikuoneka ngati njira yothawira m’ndende muno.’” Igbor anapitiriza kuti: “Zoonadi, dziko latsopano [ndi] ‘njira yothawira’ m’dziko loipali.”

Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera pothandiza abalewa komanso mabanja awo. Tikudziwa kuti nthawi zonse Yehova aziwapatsa mphamvu zimene akufunikira.—Aefeso 3:20.

a N’zovuta kudziwiratu tsiku lenileni limene khoti lidzapereke chigamulo