Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pamwamba (kuyambira kumanzere kupita kumanja): M’bale Nikolay Anufriyev; M’bale Eduard Merinkov ndi mkazi wake Valentina; M’bale Gennadiy Polyakevich komanso M’bale  Aleksandr Prilepskiy

M’munsi (kuyambira kumanzere kupita kumanja): M’bale Viktor Shchannikov ndi mkazi wake Viktoria; M’bale Gennadiy Skutelets komanso M’bale Aleksandr Vorontsov ndi mkazi wake Yelena

20 JANUARY, 2022
RUSSIA

Abale 7 a Ku Russia Akupitiriza Kupeza Mphamvu Chifukwa Chodalira Yehova

Abale 7 a Ku Russia Akupitiriza Kupeza Mphamvu Chifukwa Chodalira Yehova

Khoti la mumzinda wa Pechora ku Komi, posachedwa lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Nikolay Anufriyev, Eduard Merinkov, Gennadiy Polyakevich, Aleksandr Prilepskiy, Viktor Shchannikov, Gennadiy Skutelets ndi Aleksandr Vorontsov. Loya woimira boma sananenebe chilango chimene akufuna kuti abalewa apatsidwe.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 28 January, 2020

    Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba 12 za a Mboni za Yehova ku Komi. M’bale Polyakevich ndi M’bale Skutelets, anawatsegulira mlandu

  2. 30 January, 2020

    M’bale Gennadiy Polyakevich anatsekeredwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu. Ndipo M’bale Gennadiy Skutelets anagamulidwa kuti akhale pa ukaidi wosachoka pakhomo

  3. 20-25  May, 2020

    Apolisi anapanikiza ndi mafunso abale ndi alongo ena a ku Pechora ndi cholinga chofuna kupeza anthu omwe angawagwiritse ntchito ngati mboni pa mlanduwu. Chifukwa choopsezedwa ndi apolisi ochita kafukufuku, m’bale wina anachita sitiroko koma panopo ali bwino

  4. 26 June , 2020

    M’bale Gennadiy Polyakevich anamuwonjezera masiku omusunga poyembekezera kuzengedwa kwa mlandu wake. Jaji ananena kuti M’bale Polyakevich anamupeza ndi mlandu “wopalamula mlandu mwadala” komanso chifukwa chonena kuti “apitiriza kutumikira Yehova ngakhale kuti akuzunzidwa ndi akuluakulu a boma”

  5. 24 August, 2020

    Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba zina 12 za abale ndi alongo

  6. 10 November, 2020

    Apolisi anatsegulira mlandu M’bale Aleksandr Prilepskiy, Aleksandr Vorontsov, Eduard Merinkov, Nikolay Anufriyev ndi Viktor Shchannikov. Ndipo mlanduwu anauphatikiza ndi mlandu wa M’bale Gennadiy Polyakevich ndi Gennadiy Skutelets

  7. 25 November, 2020

    M’bale Gennadiy Polyakevich atasungidwa kwa masiku 300 poyembekezera mlandu wake, anamasulidwa n’kuikidwa pa ukaidi wosachoka pakhomo

  8. 27 January, 2021

    M’bale Gennadiy Skutelets anamasulidwa, atakhala pa ukaidi wosachoka pakhomo kwa masiku 363

Zokhudza Abalewa

Tili ndi chikhulupiriro kuti abale athu adzapeza madalitso panopo komanso m’tsogolo chifukwa chokhulupirira ubwino wa Yehova.​—Salimo 27:13.