20 JANUARY, 2022
RUSSIA
Abale ndi Alongo a mumzinda wa Karpinsk Ali ndi Chikhulupiriro Cholimba Chifukwa Chodalira Yehova
Khoti la mumzinda wa Karpinsk, m’chigawo cha Sverdlovsk, posachedwa lipereka chigamulo pa mlandu wa Mlongo Darya Dulova ndi Venera Dulova, M’bale Aleksandr Prianikov ndi mkazi wawo, Mlongo Anastasiya Prianikova ndi Mlongo Svetlana Zalyaeva. Loya woimira boma sananenebe kuti akufuna kuti anthuwa apatsidwe chilango chotani.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
27 January, 2020
Khoti linanena kuti linapeza M’bale Aleksandr Prianikov, Mlongo Darya Dulova ndi Mlongo Venera Dulova kuti ndi olakwa pa mlandu winanso
February 2020
M’bale Aleksandr Prianikov, Mlongo Darya Dulova ndi Mlongo Venera Dulova, anawatsegulira mlandu wachiwiri
30 March, 2020
Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba za anthuwa ndipo analanda zinthu ngati mafoni, matabuleti ndi malaputopu
19 May, 2020
Mlongo Anastasiya Prianikova ndi Mlongo Svetlana Zalyaeva anaphatikizidwanso pamlanduwo. Alongo awiriwa anauzidwa kuti sakuloledwa kuchoka m’dera lawo
29 April, 2021
Mlandu unayamba kuweruzidwa
Zokhudza Anthuwa
Ngakhale kuti abale ndi alongo athu akupitirizabe kumangidwa m’dziko la Russia, ndi zolimbikitsa kwambiri tikaona mmene Yehova akuwathandizira komanso kuwalimbikitsa. Chikhulupiriro chawo chomwe chikuyesedwa, chikuthandiza kuti dzina la Yehova lipatsidwe “ulemerero ndi ulemu.”—1 Petulo 1:7.