Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere: Mlongo Yuliya Miretskaya, Elvira Gridasova, Yevgeniya Lagunova, Tatyana Budenchuk ndi Nadezhda German ali kunja kwa ndende ya Orenburg mu February 2020

23 JUNE 2021
RUSSIA

Akazi a Abale Amene Amangidwa ku Russia Akudalira Yehova Kuti Apirire Mavuto Aakulu

Akazi a Abale Amene Amangidwa ku Russia Akudalira Yehova Kuti Apirire Mavuto Aakulu

Pali mavuto ena amene amabwera ngati abale amene amangidwa ku Russia asiya akazi kapena ana. Akazi awo ndi ana awo amawasowa komanso amavutika. Akazi 10 a abale amene amangidwa analemba kalata n’kuisainira onse yopita kwa akuluakulu a boma yofotokoza mosapita m’mbali mmene akumvera. M’kalatayo analemba kuti: “Takulemberani kalatayi pofuna kukulirirani chifukwa cha mavuto athu. Anthu amene timawakonda kwambiri . . . mwawatsekera chifukwa choti iwowo ndi ifeyo pamodzi ndi ana athu komanso anzathu timawerenga malamulo a m’Baibulo komanso kupemphera kwa Mulungu.”

Alongo angapo anafotokoza mavuto osiyanasiyana amene amakumana nawo chifukwa choti amuna awo amangidwa komanso mmene Yehova akuwathandizira kuti apirire.

N’zovuta Kulankhula Nawo Kapena Kukawaona

Alongo ambiri sangathe kulankhula pa foni ndi amuna awo chifukwa cha mavuto osiyanasiyana. Makalata amene amawalembera amatenga nthawi yaitali ndipo nthawi zina sawapatsa n’komwe.

Mwamuna wa mlongo Yevgeniya Lagunova dzina lake Feliks Makhammadiyev, anamangidwa kwa zaka ziwiri. Pankapita nthawi yaitali osalankhulana naye. Mlongoyu ananena kuti zinali zovuta kwambiri kudziwa ngati ali bwino kapena ayi komanso ngati kusalandira makalata kukumuchititsa kumva ngati waiwalidwa.

Akazi ambiri amayenda maulendo ataliatali kuti akaone amuna awo. (Onani tchati chakuti “Maulendo Amene Akazi Amayenda Pokaona Amuna Awo.”) Mwachitsanzo, Mlongo Yevgeniya anafotokoza kuti: “Ndinayenda pagalimoto ulendo wa makilomita oposa 800 kuti ndikaone mwamuna wanga kundende.” Ankayenda pafupifupi masiku atatu kapena 4 kuti apite kukaona mwamuna wake n’kubwerera. Alongo ena amayenda pa galimoto mtunda wa makilomita 1000. Akafika kundendeko amadikiranso pamzere wautali kwambiri.

Mwamuna wa mlongo Irina Christensen, dzina lake Dennis, anali woyamba kumangidwa pamene dziko la Russia linaletsa ntchito yathu mu 2017. Mlongoyu amayenda mtunda wa makilomita 200 kuchoka kwawo ku Oryol kuti akaone mwamuna wakeyo kundende ya ku Lgov. Iye anati: “Ulendo wa kundende ndi wovuta, wotopetsa komanso wosokoneza maganizo. Ndimafunika kunyamuka 3:30 m’mawa kuti ikamakwana 8 koloko m’mawa ndikhale nditafika n’kupereka zikalata zimene amafuna. Kenako ndimakadikira m’galimoto mpaka 11 koloko pamene amalola kuona anthu.” Atafunsidwa chimene chimamuthandiza kupirira, Irina anati: “Ndimapemphera kwambiri kwa Yehova kumupempha kuti andithandize ineyo komanso Akhristu anzanga amene ali pafupi, amene ali kundende komanso apadziko lonse.”

Amasowa Ocheza Nawo

Mlongo Nadezhda German wakhala yekha popanda mwamuna wake Gennadiy kwa zaka zoposa ziwiri. Mofanana ndi alongo ena amene amuna awo amangidwa, iye amasowa wocheza naye. Koma Nadezhda anati: “Anthu a mumpingo wathu amangokhala ngati anthu a m’banja langa. Zimachita kuonekeratu kuti amandikonda ine ndi mwamuna wanga ndipo amatisamalira.”

Mlongo Yuliya Miretskaya, amene mwamuna wake, Aleksey ali limodzi ndi Gennadiy kundende anati: “Abale ndi alongo amatithandiza ntchito zapakhomo. Ndi zolimbikitsa kwambiri kuona kuti pali anzanga odalirika amene angandithandize.”

Kulera Ana

Mlongo Tatyana Budenchuk akulera yekha ana awiri chifukwa choti mwamuna wake Aleksey anamangidwa mu September 2019. Iye anati: Anawa amaganizira kwambiri madalitso athu komanso zimene Yehova watipatsa ndipo izi zimatilimbikitsa kwambiri. Amadziwa kuti mavutowa ndi a kanthawi kochepa ndipo iyi ndi nthawi yoti tisonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova ndipo timamudalira.”

Mlongo Natalya Filatova akuleranso yekha ana 4 chifukwa choti mwamuna wake Sergey Filatov anamangidwa mu March 2020, ndipo anaweruzidwa kuti akhale kundende zaka 6. Pofotokoza za anawo iye anati: “Ndimaona kuti amawasowa bambo awo ndipo amada nkhawa poganiza kuti aliko bwanji. Amafotokoza zimene amatchula m’mapemphero. Mwana wanga wamkazi wamng’ono kwambiri amakonda kulembera makalata bambo ake n’kumawauza kuti asamade nkhawa chifukwa tonse tili bwinobwino. Koma zikanakhala bwino kwambiri akanabwera n’kumadzakhala nafe.”

Banjali limayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizikhala moyo wosafuna zambiri. Natalya anati: “Taphunzira kugwiritsa ntchito bwino ndalama osati kumangogula zinthu zosafunika kwenikweni. Ndalama zimene timapeza n’zokwanira kupeza zinthu zofunika kwambiri pa moyo.”

Kulimbitsa Chikhulupiriro Chawo

Ngakhale kuti alongowa akukumana ndi amavuto onsewa, amayesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chawo popitiriza kuchita zinthu zokhudza kulambira. Yuliya anati: “Ndimayesetsa kuti ndizichita zinthu zonse. Tingoti ndimaphunzira kuti ndipeze mfundo zothandiza anthu awiri. Chifukwa ndikamalankhula ndi Aleksey, ndimayesetsa kukumbukira mfundo zikuluzikulu zimene ndaphunzira n’kumufotokozera. Nadezhda anati: “Palibe vuto limene sitingathe kulimbana nalo mothandizidwa ndi Yehova. Panopa nthawi iliyonse ndimaona kuti ubwenzi wanga ndi Mulungu ndi wolimba kwambiri. Ndimamva ngati ndine kamwana kamene kali m’manja mwa bambo ake omwe ndi amphamvu zopanda malire. Ndimamva bwinonso ndikamathandiza anthu ena.”

Natalya ananenanso kuti: “Ndimakumbukira zimene mlongo wina ananena: ‘M’gulu la Mulungu, palibe amene safuna kulimbikitsidwa, ndipo palibenso amene sangathe kulimbikitsa anthu ena. Ndimamva bwino kwambiri ndikakwanitsa kulimbikitsa munthu wina.” Natalya anapitiriza kuti: “Kukhala ndekha popanda mwamuna wanga n’kovuta chifukwa zimanditopetsa komanso kundisokoneza maganizo, koma sindimangokhalira kudzimvera chisoni. Sindifuna kumupatsa mpata Satana woti andifooketse!”

Abale ndi alongo padziko lonse amayamikira kwambiri zimene mabanja a abale amene ali kundende za ku Russia ndi m’mayiko ena akuchita. Iwo akupereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yopirira. Tikudziwa kuti Yehova amayamikira kwambiri anthu amenewa omwe ndi ‘amtengo wapatali kwa iye.’​—Yesaya 43:4a.