FEBRUARY 17, 2020
RUSSIA
Alonda a Ndende Anamenya Abale 5 Mumzinda wa Orenburg ku Russia
Pa 6 February 2020, mumzinda wa Orenburg ku Russia, alonda a ndende ya Penal Colony No. 1 anamenya ndi zibonga abale 5 modetsa nkhawa. Abalewa ndi: Aleksey Budenchuk, Gennadiy German, Roman Gridasov, Feliks Makhammadiyev, ndi Aleksey Miretskiy. M’bale Makhammadiyev anagonekedwa kuchipatala atathyoledwa nthiti, kuvulazidwa mapapo komanso impso. M’bale Budenchuk, German, Gridasov, ndi M’bale retskiy atamenyedwa anaikidwa m’selo yozunzirako anthu powanamizira kuti anapalamula milandu. Ina ya milandu yomwe akuimbidwa ndi yakuti ankasuta fodya, zomwe ndi zodabwitsa kwambiri chifukwa a Mboni za Yehova sachita zimenezi.
Monga mmene nkhani ina inafotokozera, pa 19 September, 2019, woweruza milandu kukhoti m’boma la Leninsky mumzinda wa Saratov dzina lake Dmitry Larin, anagamula kuti abale 5 amenewa ndi olakwa pamodzi ndi M’bale winanso dzina lake Konstantin Bazhenov. Abalewa anagamulidwa kuti akakhale m’ndende kwa zaka kuyambira ziwiri mpaka zitatu ndi hafu. Pa 20 December, 2019, khoti la ku Saratov linakana apilo yomwe abalewa anapanga. Patatha milungu ingapo, abale onse 6 anawapititsa kundende. M’bale Bazhenov anatumizidwa kundende yotchedwa Penal Colony No. 3 yomwe ili m’dera la Ulyanovsk. Choncho m’baleyu sanamenyedwe limodzi ndi enawo.
Abale 5 amenewa anamenyedwa atangofika kundende yotchedwa Penal Colony No. 1 pa 6 February 2020. Madokotala sanawathandize mpaka tsiku lotsatira pamene M’bale Makhammadiyev anatentha thupi kwambiri komanso mkodzo wake unapezeka ndi magazi. Akuluakulu a ndende anaitana ambulansi pambuyo pokakamiza M’bale Makhammadiyev kuti asaine chikalata chosonyeza kuti “anateleleka m’bafa n’kugwa.” M’bale Makhammadiyev anagonekedwa m’chipatala ndiponso anapangidwa opaleshoni kuti amuchotse madzi omwe anadzadza m’mapapo ake. Madokotala anapezanso kuti M’bale Makhammadiyev analenguka ndi njala chifukwa choti akuluakulu oyang’anira ndendeyo anamulanda chakudya chapadera chimene m’baleyu amafunikira kudya chifukwa cha matenda omwe ali nawo.
Tikumva chisoni kwambiri chifukwa cha nkhanza zoopsa zimene abale athu ku Russia akuchitidwa. Komabe, tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kuwathandiza kuti apirire mokhulupirika.—Afilipi 1:27, 28.